Chichewa

Iphani udzu m’munda ndi mankhwala

Padamu limodzi lokha la mamita 20 mulitali ndi 18 mulifupi wakololapo nsomba zolemera makilogalamu 300 atazidyetsera kwa miyezi 5 chakudya cha nsomba chochokera m’dziko la Zambia.

Pamene nyengo yolima ndi mvula ikuyandikira, alimi ena ozitsata ali pa kalikiliki kugula mankhwala opha udzu kuti adzapopere m’minda mwawo akazangobzala mbewu zawo.

Malinga ndi mwini wake wa Edfa Agro-dealers ku Zomba Keston Nzeka, pakadalipano mankhwala amene akuyenda malonda ndi Harness komanso Round Up amene akathiridwa m’munda udzu umayimika manja.

Iye adati kwa alimi ambiri amene akhala akugula mankhwalawa m’sitolo mwake, nyengo yokolola ikafika amamwemwetera chifukwa cha ndalama zimene amateteza popalira.

Alimi ngati Kaunda akuti nsomba zimatulutsa ndalama zochuluka pamalo pochepa

Nzeka adatinso botolo limodzi la Harness amagulitsa K4 500 limene limatha kupoperedwa pamunda osachepera hekitala imodzi pamene mankhwala a Round Up amagulitsa K6 500 ndipo amathiridwanso pamunda wosachepera hekitala.

“Pamenepatu mlimi amateteza ndalama chifukwa kupalira hekitala imodzi ndi khasu pakhoza kulowa ndalama zambiri komanso amateteza mbewu chifukwa nthawi zina popalira mlimi amatha kukhapa mbewu monga chimanga chimene chikakhapidwa moyo wake umakhala kuti wathera pomwepo,” adatero iye.

Katswiri ogulitsa zipangizo za mbewuyo adati alimi ena amaopa kupopera mankhwalawa poganiza kuti awononga nthaka.

“Alimi ena amaganiza kuti mankhwalawa amapha chilengedwe m’munda koma si choncho ayi chifukwa ntchito yawo ndi kuchedwetsa udzu chabe kuti uyambe kumera mochedwa kupereka mpata kwa chimanga ndi mbewu zina kuti zizikula mwa ufulu,” adatero iye.

Wa malondayo amene sitolo yake ili kufupi ndi Zomba Community Centre Ground komanso Admarc walangiza alimi kuti pamene mvula ikununkhira alimi agule zipangizo za ulimi monga mankhwala kwa ogulitsa mbewu ovomerezeka ndi boma.

“Ubwino wogula mankhwala kwa anthu ovomerezeka ndi woti ngati mankhwalawo apezeka ndi vuto mlimi amakhala ndi ufulu wodzabweza koma kugula paliponse kumadzetsa chisokonezo pa ulimi,” adatero iye.

Mlangizi wa zaulimi pa nkhani ya mankhwala amenenso ndi mwini wake wa Chilumba Farm Lipherani Mkhupera adati kupha udzu ndi mankhwala kumachepetsa mpikisano pakati pa mbewu ndi tchire.

Malinga ndi Mkhupera, mavuto amene amakhalapo kwambiri pogwiritsa ntchito mankhwalawa ndi akuti alimi amathira nthawi yosayenera. Mwachitsanzo, iye adati kuthira pamene tchire lakula kale m’munda.

“Ndi bwino kuti alimi asanapopere mankhwala azifunsa alangizi a zaulimi kudera lawo pa njira zoyenera za mankhwalawa,” adatero iye.

Mkhupera adagwirizana ndi Nzeka kuti ngati mankhwala agwiritsidwa moyenera amapulumutsa ndalama zochuluka zimene akanalipira aganyu.

Mmodzi mwa alimi amene akhala akugwiritsa ntchito mankhwala kwa zaka zingapo Richard Chilele wa ku Namadidi m’boma la Zomba adati akusiyanitsa kwambiri phindu limene amapeza akakolola pofanizira ndi kale mmene amadalira anthu a ganyu.

“Chofunika alimi atengepo gawo pogwiritsa ntchito njira za makono za ulimi kuti ulimi ukhale nsanamira ya chuma cha dziko lino,” adadatero iye.

Malingana ndi Chilele, botolo la lita imodi ya mankhwala amayisungunula m’chopopera mankhwala cha malita 20.

“Pa ekala imodzi ndimapopera mabotolo atatu ndipo pa hekitala ndimapopera mabotolo anayi,” adatero iye.

Mchikumbeyu adati amapopera mankhwalawa pakangotha masiku anayi akangobzala chimanga.

“Zimenezi zimathandiza kuti udzu usaphuke m’munda kupereka danga kwa chimanga kuti chikule motakasuka,” adatero Chilele.

Related Articles

Back to top button