Chichewa

Katemera wa covid ayamba

Listen to this article

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera Lachinayi adalandira katemera wa matenda a Covid 19 pachipatala chapadera cha matendawa chomwe achikhazikitsa kunyumba ya boma ku Zomba.

Chakwera adafika kumaloko ndi mkazi wake Monica. Iye adavomera kuti abaidwe wachipatala atamufotokozera za ubwino wa katemerayo. Adavula jekete ya suti yake kuti abaidwe.

“Inde ndamvetsa, ndipo ndakonzeka,” adatero Chakwera.

Chakwera adalandira katemera just Zomba

Ndipo wachiwiri wake Saulos Chilima adalandira katemerayo pachipatala cha boma ku Mzuzu.

Ziphaliwali zidali ng’aning’ani, kwinaku mvula yambiri ili mkati, Chilima adailowa mvulayi pokalandira katemera.

Chilima adati akuyembekezera kuti zomwe achita atsogoleriwa pobaitsa katemerayu zipangitsanso ena kuchita chimodzimodzi mtsogolomu chifukwa katemerayu ngwabwinobwino.

“Ndikufuna ndilimbikitse aliyense yemwe ali pa mndandanda wolandira katemerayu kuti atero ndithu komanso ndikupempha andale, a mipingo komanso mafumu kuti agwire ntchito limodzi ndi boma pofalitsa uthenga wolondola wokhudza katemerayu,” adatero Chilima.

Nduna ya zaumoyo Khumbize Kandodo Chiponda adati katemerayo si wokakamiza ngakhale n’kofunika kuti anthu abaitse mwaunyinji kuti akhwimitse chitetezo chawo ku matendaww.

“Kulandira katemerayu ndi njira imodzi yodzitetezera chifukwa amagwira ntchito ndi chitetezo cha m’thupi kuti ngati munthu watenga kachilomboko, kasamakhalitse m’thupi mwake. Choncho, onse oyenera kulandira katemerayu kalandireni,” adatero Kandodo.

Izi zili apo, mafumu ena ati anthu ena m’madera mwawo sadakonzekere kulandira katemerayo chifukwa sadalandire uthenga wokwanira okhudza katemerayo moti akadali ndi zikhulupiliro zolakwika.

Mfumu Maseya ya ku Chikwawa yati mwa anthu 100 aliwonse, anthu 80 akuonetsa kuti sakufuna katemerayo pomwe anthu 20 akupenekera ngati adzalandire nawo.

“Anthu akukhulupilirabe kuti ukalandira katemera ameneyu ndiye kuti walandira chirombo choopsa cha 666, ena akuti ndiye kuti sudzaberekanso pomwe ena akukhulupilira kuti katemerayo ngofupikitsa moyo,” watero Maseya.

Nayo mfumu Chingalire ya ku Lilongwe yati n’zokayikitsa kuti anthu a mdera lake adzalandira katemerayo chifukwa zikuonetsa kuti palibe uthenga omwe adalandirako okhudza katemerayo kotero anthuwo akukhulupilira mphekesera zoyipa.

“Kuno ambiri akuti awa ndi matenda a anthu olemera a m’tauni. Ena akuti mwina pali katemera muwiri, wina woti adzabayane akuluakulu kenako woipa wa anthu wamba,” adatero Chingalire.

Iye wati anthu ake akunenetsa kuti matupi awo adapima kale ndi mavuto osiyanasiyana ndiye sakuona chachilendo ndi matenda a Covington 19 kuti mpaka akakhale ndi phuma ndi katemera yemwe sakumudziwa bwino.

Mafumu awiriwa agwirizana pa mfundo yoti anthu ambiri akana katemerayo chifukwa sadalandire uthenga mokwanira kuti adziwe zowona zake zoipa ndi zabwino.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaumoyo la Malawi Health Equity Network, (Mhen) George Jobe adachenjeza kuti boma likuyenera kupanga machawi potuma akadaulo odziwa za makhwala kuti apange mauthenga ndi kumwaza paliponse katemerayo asadafike.

“Zonse zomwe zikumvekazi n’zamaluwa chifukwa palibe wa zaumoyo amene wapereka uthenga oterowo choncho boma likuyenera kuchita machawi ndipo lisalole andale kulowererapo chifukwa sadziwa za zaumoyo ndiye asokeretsa anthu,” adatero Jobe.

Iye adati mmbuyomo kudagwapo miliri yosautsa yomwe idagonjetsedwa ndi katemera yemwenso pachiyambi amakanidwa ndi anthu chifukwa chazikhulupiliro.

“Olo unduna wa zaumoyowo ukudziwa kuti anthu sangangofikira kuvomereza pokhapokha atalandira uthenga omveka bwino komanso ochokera kwa akadaulo enieni a zamankhwala,” adatero Jobe.

Anthu 360 000 akuyembekezeka kulandira katemera koyambirira. Awa ndi a zaumoyo, apolisi, asilikali, aphunzitsi, oyang’anira ndende, atolsnkhani komanso okalamba ndiwo alandire katemerayu.

Mlembi wa unduna wa zaumoyo Dr Charles Mwansambo wati boma ndi mabungwe komanso maiko omwe amalithandiza akhala akuonjezera katemerayo mpakana anthu okwana 11 miliyoni atalandirs.

Anthu atatu oyambilira kupezeka ndi Covid 19 m’dziko muno adapezeka pa 2 April 2020 patatha sabata ziwiri zokha kuchoka pomwe bungwe la zaumoyo padziko lapansi la World Health Organization (WHO) lidalengeza kuti Covid 19 ndi mliri.

Pofika pa 31 December 2020, matendawa adali atapha anthu 189 m’dziko muno koma pofika Lachitatu, chiwerengerocho chidali pa 1 074.

Related Articles

Back to top button
Translate »