Chichewa

Khrisimasi ya maluzi

Listen to this article

 

Kwangotsala masiku anayi kuti chisangalalo cha Khrisimasi chifike pachimake koma ochita bizinesi zosiyanasiyana akudandaula kuti sizikudziwika kuti nyengoyi yafikadi malingana ndi momwe akuvutiramalonda.

Ochita malonda m’misika ikuluikulu ya m’mizinda ya Mzuzu, Lilongwe ndi Blantyre ati pomafika nthawi ngati zino m’zaka zammbuyomu, bizinesi zawo zimayenda kwambiri moti ena amapikula katundu kawiri kapena katatu pasabata, koma chaka chino akuti zimenezo kulibeko.

Ngakhale  m’sitolo zikuluzikulu monga za Shopright malonda sakuyenda kwenikweni
Ngakhale m’sitolo zikuluzikulu monga za Shopright malonda sakuyenda kwenikweni

“Anthu ena omwe adapikulira katundu mwezi wa November mpaka lero akadagulitsa yemweyo, malonda akuvuta. Zoti ndi December malonda amayenda ayi ndithu, osadziwika n’komwe,” adatero Mlembi wa ochita malonda mumsika wa mzinda wa Mzuzu Justin Hara pocheza ndi Tamvani Lachitatu.

Iye adati momwe zikuonekera, anthu alibe ndalama kapena ndalama ali nazo koma akuopa kuti akazisakaza adzavutika, malingana ndi momwe chuma chikuyendera.

“Tikuganiza kuti ambiri akulingalira za mafizi akwerawa komanso akuti akaona momwe chuma chikuyendera akuda nkhawa kuti akadya ndalama adzakhala pamavuto aakulu. Magulitsidwe ake akungokhala ngati talowa kale January,” adatero Hara.

Wa pampando wa msika waukulu mumzinda wa Lilongwe, George Banda, adati zikuoneka kuti chaka chino mumsika n’zamalodza zomwe sizidachitikepo n’kale lonse.

“Malonda asanduka ngati muja amachitira a minibasi kuchita kuthamangira munthu kunjira kumukokera pamalonda, kutanthauza kuti bizinesi yafika povuta. Zikumatheka ena mpaka kuweruka momwe adabwerera ndithu,” adatero Banda.

Mkuluyu adapereka tsatanetsatane wa momwe ochita malondawa amatcherera bizinesi zawo polinganiza katundu yemwe amakonda anthu akumudzi ndi apantchito zomwe adati sizikutheka chaka chino.

“Timatchera kuti mwezi wa November timapikula zomwe amakonda anthu akumudzi ndipo timayembekezera kuti tikalowa December katundu ameneyu amakhala atatha chifukwa anthu ambiri akumudzi amadzaguliratu zinthu kuti azikagwira ntchito zina.

“Tikamalowerera mkati mwa December, timakapikula za anthu apantchito m’tawuni, koma pano ambiri tikadali ndi katundu woyambirirayo,” adatero Banda.

Kaphidigoliyu sadasiye anthu a kummwera komwe akuti nako zinthu sizikuyenda momwe zimakhalira mmbuyomu.

Wapampando wa ochita malonda mumsika waukulu ku Blantyre, Himon Amanu, adati nyengo ngati ino mumsinkawu mumakhala gulu la mundipondera mwana, koma chaka chino anthu akuyenda mosacheukacheuka.

“Zinthu zatembenukiratu, palibe chikuyenda. Anthu afumbata ndalama zawo ndipo sakufuna kuononga, ayi,” adatero Amanu.

Zonsezi n’chifukwa cha kuchepa mphamvu kwa ndalama ya kwacha.

Chaka chino chokha kuchoka mu March ndalama ya kwacha yagwa kuchoka pa K435 posinthanitsa ndi ndalama ya Amerika ya dollar kufika pa K612 mwezi uno wa December.

Kuchepa mphamvu kwa ndalamayi kwadza chifukwa chakuti dziko lino silikugulitsa malonda kumaiko akunja mokwanira. Kupatula fodya, shuga, tiyi, thonje ndi mbewu zina, palibe malonda omwe dziko lino likudalira kuti akhazikitse kwacha pansi.

Malingana ndi odziwa za chuma, mphamvu ya ndalama imakhazikika ngati dziko likupanga katundu wabwino yemwe maiko ena akumukhumba.

Dziko la Malawi limadalira mabungwe ndi maiko akunja omwe amapereka thandizo la ndalama, zomwe zimapangita kuti ndalama ya kwacha isakhale pendapenda.

Ndiye pomwe mabungwewa adati asiya kuthandiza dziko lino kaamba ka “kusolola ndalama” m’boma, mavuto akhala aakulu m’dziko muno.

Chinanso chomwe chikupangitsa kuti ndalama ya kwacha iguge ndi chakuti dziko la Amerika chuma chake chikuyenda bwino kwambiri, zomwe zapangitsa kuti ndalama ya dollar ikhale yamphamvu kuposa ndalama zina monga ndalama ya pound.

Izi zapangitsa kuti maiko ambiri osauka akhale pachiopsezo chifukwa chuma chawo sichikuyenda bwino.

Bungwe la International Monetary Fund (IMF) lomwe ndi limodzi la mabungwe omwe amathandiza dziko lino ndi ndalama, m’sabatayi lati dziko la Malawi liyenera kukhwimitsa ndondomeko ya zachuma chake kuti anthu osolola ndalama asiye.

Bungwelo latinso boma lichepetse kusakaza ndalama pazinthu za zii zopanda mutu, kuonjezera kuti boma likuyenera kuchitapo kanthu kuti zinthu zitsike mtengo poonetsetsa kuti pali mfundo zabwino zoongolera chuma.

Koma bungwe la amipingo la Public Affairs Committee (PAC) lati anthu asaiwale cholinga cha chikondwererochi poganizira zosakaza ndalama.

Wapampando wa bungweli, mbusa Felix Chingota, wati nyengoyi ndi yokumbukira kubadwa kwa mpulumutsi Yesu Khrisitu osati kungolingalira “zonjoya” basi.

“Inde, ndi nyengo yachisangalalo anthu akuyenera kusangalala, koma asaiwale cholinga cha chisangalalocho chifukwa ena amapezeka kuti chisangalalo chomwecho avulala nacho mwinanso kutaya nacho moyo mmalo mopata moyo mwa Yesu Khrisitu,” adatero Chingota.

Iye adati nkhawa zoti pali ndalama kapena palibe zisakhale chipsinjo kwa anthu koma atenge nyengoyi ngati yophathana ndi Mpulumutsi wawo.n

Related Articles

Back to top button