Chichewa

Kodi Idrissa Walesi akutani mu Mozambique?

Listen to this article

 

Mu 2012 ku Mighty Wanderers kudatchuka wosewera wa kumbuyo, Idrissa ‘baba’ Walesi. Atangotchuka, Walesi adasowa ndipo zidamveka kuti wakwawira ku Mozambique. Chipitireni mu 2014, Walesi adachita zii! Kodi akusewera? Kapena wayamba geni? BOBBY KABANGO adamupeza mumzinda wa Nacala Provincia m’dziko la Mozambique ndipo acheza motere;

Idrissa ‘Baba’ Walesi ulipo?

Ah achimwene, ndilipo ine. Mwasowatu…

Ukutani m’dziko la Mozambique?

Walesi akudya bwino ku Mozambique
Walesi akudya bwino ku Mozambique

Pajatu chibwerereni kuno mu 2014 ntchito yanga ndi yampira basi. Kuchokera pa nthawiyo ndakhala ndikusewera timu ya Desportivo mpaka lero pamene ndasintha timu.

Koma umasewera nthawi yonseyi? Kapena ku training kokha?

Haha mwandinyozatu achimwene. Ndakhala ndikusewera pafupifupi gemu iliyonse. Chaka changothachi adandisankha ku timu kwathu kuti ndatchinga bwino kumbuyo.

Chibwerereni ku Mozambique, timu yako yasewera bwanji?

Chaka chathachi ndiye sizidayende, tathera pa nambala 12 ndi mapointi 29.

Chachitika nchiyani kuti uchoke ku timuyi?

Tidali pa mgwirizano wa zaka ziwiri, mgwirizano watha koma adandipempha kuti ndisewererebe timuyi koma ndakana chifukwa timu yomwe ndapita panoyi idandilonjeza zochuluka.

Timu yanji? Ndipo uzilandira zingati?

Ferroviario De Nacala yomwe idathera pa nambala 8. Achimwene mpaka ndinene malipiro? Aah ayi koma inu nokha mutha kudziwa koma musalembe. Koma ndayamba timu imeneyi chaka chatha ndipo tili pa mgwirizano wa chaka chimodzi kuchokera pa 26 February 2016.

Ndiye wati umachita bwino ku timu yako? Nanga bwanji samakutenga ku Flames?

Ngati adandisankha kukhala wosewera bwino ndiye kuti ndimasewera bwino. Nkhani ya Flames inayamba kundivuta kuyankha tsopano chifukwa nthawi zonse bambo anga akhala akundifusa zotengedwa ku Flames. Koma ndimawayankha mwachidule kuti ndi posachedwapa koma posachedwa pake sipafika, ndiye kuyambira nthawiyo, ndimangoyang’ana chitsogolo basi. n

Related Articles

Back to top button
Translate »