Chichewa

Kunalibe kubera mu 2015—Maneb

Listen to this article

 

Wapampando wa bungwe loona za mayeso la Malawi National Examinations Board (Maneb) John Saka wati bungweli ndi lokondwa kuti m’chaka cha 2015 mayeso onse amene bungweli limayendetsa adayenda bwino chifukwa padalibe zobera.

Polankhula kwa atolankhani ku Sunbird Mount Soche mumzinda wa Blantyre Lachiwiri, Saka adati ali ndi chikhulupiriro chonse kuti bungweli lathetsa kubera mayeso.

Akuti zobera mayeso zikuchepa
Akuti zobera mayeso zikuchepa

Iye adati pamayeso onse atatu a Primary School Leaving Certificate of Education (PSLCE), Junior Certificate of Education (JCE) ndi Malawi School Certificate of Education( MSCE) lidakumana ndi vuto limodzi lokha lokhudza kubera mayeso pa JCE.

Saka adati: “Iyi ndi nkhani yosangalatsa kwambiri poyang’anira momwe zakhala zilili pankhani yobera mayeso m’dziko muno zaka zingapo zapitazo.

“Ndife okondwa kuuza dziko lonse kuti mayeso a m’chaka cha 2015 ayenda bwino kwambiri ndipo sanabedwe. Zotsatira zimene zidatuluka ndi zoona zenizeni za mmene ophunzira aliyense adalembera mayeso ake. Tipitiriza kuonetsetsa kuti mayeso asadzabedwenso.”

Wapampandoyo adati izi zidatheka chifukwa cha mgiwrizano umene ulipo pakati pa magulu osiyanasiyana amene amatengapo mbali poyendetsa ntchito za mayeso m’dziko muno monga apolisi, asilikali a nkhondo, aphunzitsi, boma ndi ena onse. Iye adaonjezera kuti chitetezo cha mapepala amayeso chakwera kwambiri chifukwa cha njira yatsopano imene idakhazikitsidwa mchitidwe wobera mayeso utafika poipa.

“Timakhala ndi malo amodzi kumene timasungako mayeso. Kumakhala apolisi ndi asilikali a nkhondo omwe amateteza malowa koma alibe mpata wolowa mkati mwa nyumbayo mwaokha. Tili okondwa kuti njirayi ikuthandiza ndipo ipitirira,” adatero Saka. n

Related Articles

Back to top button