Chichewa

Sabuside yayamba ndi njengunje

Listen to this article

 

Pulogalamu ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo ya sabuside ya chaka chino yayamba koma zokhoma zilipo zambiri kuyerekeza ndi zaka zammbuyomu, nduna ya zamalimidwe Allan Chiyembekeza yavomereza.

Polankhula ndi Uchikumbe, Chiyembekeza adati pulogalamuyi yayamba ndi jenkha chonchi kaamba ka mavuto ena monga a zachuma chifukwa boma tsopano likudzidalira palokha pachuma chake.

Ndunayo idati ngakhale ntchitoyi yayamba ndi mavuto oterewa, Amalawi asataye mtima chifukwa boma kudzera muundunawo likudzipereka kuti alimi asavutike.

Anthu kudikira kugula zipangizo zotsika mtengo chaka chatha
Anthu kudikira kugula zipangizo zotsika mtengo chaka chatha

“Tikuvomereza kuti zinthu sizidayambe bwino koma sizikutanthauza kuti zinthu zaipiratu ayi chifukwa padakalipano zipangizo zayamba kale kupita m’madera moti alimi asataye mtima zinthu ziyenda,” adatero Chiyembekeza.

Ndunayo idati polingalira mavuto a mayendedwe nthawi ya mvula, ntchitoyi yayamba m’madera ovuta kufikira m’dziko lose la Malawi polingalira kuti mvula ikayamba m’madera oterewa galimoto zonyamula zipangizozi zimatitimira kapena kugwa m’matope.

“Tayambapo makamaka m’madera ovuta kufikira mvula ikagwa. Panopa madera ambiri oterewa alandira kale zipangizo moti alimi akungodikira makuponi ogulira kuti akagule,” adatero Chiyembekeza.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaulimi wa Civil Society Agriculture Network (Cisanet) Tamani Nkhono Mvula adati boma lachita bwino kubwera poyera nkunena momwe pologalamuyi ikuyendera kuti alimi azidziwiratu zochitika.

Nkhono adati kawirikawiri zinthu zimaonongeka chifukwa chobisa momwe zinthu zilili zomwe zimachititsa kuti alimi azidzidzimutsidwa nthawi yothaitha zinthu zitasokonekera kale.

“Pamenepa ife tiyamikire boma chifukwa lapanga zazikulu kubwera poyera. Nthawi zambiri chilungamo ngati ichi chimabisidwa chifukwa cha ndale koma mapeto ake zinthu zimasokonekera,”adatero Nkhono.

Iye adati alimi panopa akhale kalikiliki mminda kuyembekeza mvula yobzalira osatengera kuti boma lalankhula bwanji chifukwa iwowo ndiwo amalima osati boma lomwe limangothandizapo.

Alimi ambiri pano ali m’minda kukonza kapansi kuti mvula ikangogwa abzale mbewu koma akuti ali ndi nkhawa chifukwa sakudziwa kuti mbewu ndi zipangizo zina ngati feteleza azipeza liti poti sadalandilebe makuponi ogulira.

Amos Dziyende ndi mmodzi mwa alimi omwe adakonza kale munda wake ndipo adati nkhawa yake ili pawiri: Mtengo wa zipangizo ndi nyengo yogulira poti mpaka lero sadalandirebe makuponi ogulira.

“Tidakonzeka koma tikumva kuti mtengo wa zipangizo chaka chino wakwera ndiye kaya zitha bwanji komanso mpaka pano makuponi sitidalandire, “ adatero Dziyende.

Panopa mvula yagunda kale m’madera ena ndipo nthawi iliyonse madzi akhala akugwa pansi kuti dzinja.

Related Articles

Back to top button