Kupherera ng’amba ndi Akalozera m’munda

 

Alangizi a zaulimi apempha alimi m’dziko muno kuti azipanga akalozera kuti ateteze nthaka, komanso kusunga chinyontho kwa nthawi yaitali m’minda yawo.

Madalitso Munthali, mlangizi wa mbewu ku Kaporo m’boma la Karonga, wauza Uchikumbe kuti mavuto odza ndi kusintha kwa nyengo atha kuchepa alimi ambiri atayamba kupanga akalozera m’minda mwawo.

Mlangiziyu adati akalozera amathandiza alimi kukolola madzi a mvula, komanso kuteteza nthaka kuti isakokololoke m’munda mwawo.

Alimi kupanga akalozera pogwiritsa ntchito chingwe

Akalozera ndi muuni wa kayendedwe ka madzi m’munda ndipo alimi amayenera kuunga mizere. Umu ndi momwe mumalimidwa milambala, yoongoledwa bwino, yomwe imachengeta nthaka podekhetsa madzi m’mizere.

“Kulima mwa chisawawa, opanda akalozera, zikuchititsa kuti nthaka izikokoloka ndi madzi a mvula.

“Zotsatira zake ndi njala chifukwa chajira chikukokoloka kusiya minda yoguga ndipo mbewu zikumauma posowa chinyezi popeza madzi amangothamangira ku mitsinje,” adatero Munthali.

Katswiriyu adalangiza alimi kupeza thandizo la alangizi a m’madera mwawo popanga akalozera.

“Osangokhala kumadikira mvula igwe mu October kapena November. Pakadalipano, mlimi wotsogola akupanga akalozera, manyowa ndi galauza,” iye adatero.

Mlangizi wina wa ku Chingale EPA m’boma la Zomba, Limbani Thangata, akuti nthaka ndi yofunika kwambiri pa ulimi choncho iyenera kutetezedwa.

“Alimi asaiwale kuti kusintha kwa nyengo kukusokoneza ntchito yathu choncho tiyenera kupanga akalozera m’munda mwawo.

“Dongosololi limathandiza kusamalira chajira poimitsa madzi n’kusunga chinyezi kwa nthawi yaitali chothandiza mbewu kuchita bwino ngakhale mvula idule,” adatero Thangata.

Mkuluyu adati kupanga akalozera ndi njira imodzi yothana ndi ng’amba kaamba koti madzi samathamanga ndipo akhala ndi nthawi yolowa pansi m’munda makamaka alimi akapanga maswale, ulimi wa m’maenje, phimbira ndi ngonyeka (box ridges).

Popanga akalozera, Thangata adati pamafunika anthu atatu, chingwe chotalika mamita 5, mitengo (ndodo) iwiri yoongoka bwino n’kutalika mamita 1.6 mpaka 2.0, chikwanje, zikhomo, hamala ndi levulo—ija amagwiritsa ntchito amisili pomanga nyumba.

Adafotokoza kachitidwe kake motere: “Anthu awiri amaima ndi ndodo zomangidwa chigwecho ndipo m’modzi amakhala pakati ndi levulo ija kuyeza. Pomwe timadzi mu levuloyo tabwera pakatikati, wa kumapeto amakhoma chikhomo ndi kusunthira komwe kuli ndime.

“Amatero mpaka kumaliza munda wonse. Malingana ndi kutsika kwa malo, akalozera amatalikirana mamita 5 kapena 10. Umu ndi momwe timaungamo milambala ija.”

M’modzi mwa alimi m’minda mwawo muli akalozera m’mudzi mwa Giliya kwa mfumu Mwaulambo m’boma la Karonga,

Jimmy Mwakila ndi mmodzi mwa alimi womwe amapanga akalozera munda mwake. Mwakila, wa m’mudzi mwa Giliya m’dera la mfumu Mwaulambo ku Karonga, adati dongosololi lamuthandiza kuti azikolola dzinthu zambiri.

“Ubwino wake wa akalozera ndi woti umapanga kamodzi basi bola osaphwasula mizere polima. Polimbikitsa milambala, ndidabzalamo udzu wa vetiva. Mlimi ofuna kusimba lokoma chaka chino apange akalozera basi,” adatero Mwakila. n

Share This Post