Nkhani

Kusakasaka maphunziro

Listen to this article

Cholinga cha mnyamatayo chidali kuyenda pansi kuchokera kwawo ku Mayani kupita ku Dedza paboma, mtunda wa makilomita 40. Iye ankalingalira kuti akafika pabomapo apeze mayendedwe kuti akafike kusukulu ya ukachenjede ya University of Malawi (Unima) ku Zomba.

Kuyenda mtunda wa makilomita 40 si masewera.

Kumbemba atangofika paboma ku Dedza

Ku Zombako, amafuna akapemphe akuluakulu a sukuluyo kuti amusungire malo ake chifukwa alibe fizi.

Iyi ndi nkhani ya Alexander Kumbemba, mnyamata wa zaka 19 yemwe adamusankhira ku Unima atapeza mapointsi 17. Iye adasankhidwa kukachita maphunziro a ukachenjede a Bachelor of Arts Theology (ukachenjede wa zachipembedzo) kuchokera pa sukulu ya St Kizito Minor Seminary. 

Ndipo mwezi wa May chaka chino, Kumbemba adakayamba sukulu, koma adasiya patangodutsa sabata zitatu chifukwa sadachite mwayi wopata ngongole ya fizi komanso adalibe ndalama ya chakudya ndi malo ogona.

Kumbemba adati malo ogona adapeza a K19 000 pamwezi pomwe chakudya chimafunika kuti azikhala ndi K30 000 pa mwezi zomwe adakanika kukwanitsa ndipo adasiya sukulu ndi kubwerera kwawo ku Chitundu ku Mayani m’boma la Dedza.

Chifukwa cha umphamwi, iye amafuna kupitirira ulendowo mpaka ku Zomba kukakambirana ndi akuluakulu a kusukuluyo kuti amusungire malo poganizira kuti mwina chaka cha mawa adzapeza fizi.

Koma mnyamatayu atayenda mtunda wautali ndithu kuchokera ku Chitundu, adakumana ndi galimoto yomwe idamuimira ndi kumnyamulako atadandaula za mavuto ake.

Adalongosola Kumbemba: “Adakandisiya pa roadblock ya Dedza pomwe ndidalongosolera apolisi bwana Dickie Chibambo za mavuto anga ndi komwe ndimapita.

“Ndimafuna kuti andipezere galimoto yaulere kuti ndikafike ku Zomba. Apolisiwa adandimvera chisoni n’kundiuza kuti ndigone kaamba koti kudali kutada.”

Iye adati a Chibambo adalumikizana ndi mnzawo a Gerald Kampanikiza yemwe ali ndi tsamba la mchezo la GCK Camera pa Facebook ndipo kudzera patsambali, amathandiza anthu ambiri osowa kuphatikizapo ophunzira a m’sukulu za sekondale ndinso za ukachenjede.

Apa a Kampanikiza sadachedwe koma kusaka thandizo la mwanayu kwa anthu akufuna kwabwino.

Ndipo polankhulapo, a Kampanikiza adati apeza thandizo loti likwanitsa kumulipirira fizi mwanayu kwa zaka zake zonse zinayi, kulipira malo ogona ndi chakudya komanso kupeza zosowa zina ndi zina pamoyo wake.

“Tathandiza ana a sukulu zaukachenjede ambiri koma enanso amene timawathandiza kwambiri ndi a ku sekondale, makamaka chaka chino,” adalongosola a Kampanikiza.

Iwo adati akuthokoza Amalawi omwe amati akamva dandaulo amabwera poyera ndi kuthandizapo anthu omwe akusoweka thandizo.

“Boma liphunzirepo kanthu kuti tisiye kumangodalira mabungwe otithandiza kuchokera kunja, kuti ngati dziko tikhonza kuyamba kumadzidalira patokha.

“Komanso boma liunikepo bwino kuti pali ana ambiri omwe akuvutika kupeza fizi, chakudya ngakhalenso malo ogona ndipo likamapereka ngongole, liziganizira zonsezi, osamangopereka fizi yokha,” iwo adatero.

Pomwe Msangulutso udapitirira kucheza ndi Kumbambe, iye adati adayamba kuvutika fizi ali kusekondale chifukwa telemu yomaliza ali Fomu 4, anthu akufuna kwambwino ndiwo adamulipirira. Pasukuluyi ankalipira fizi ya K115 000 pa telemu.

“Nditapita kukoleji, ndimaona ngati ndipeza mwayi wa fizi chifukwa ndidalembera nawo ku bungwe la Higher Education Students Loans and Grants Board koma sadanditenge,” adalongosola Kumbemba.

Iye adati adawauza amalume ake omwe nawonso panthawiyo zidali zitawathina.

“Nditabwerera kumudzi ndimasaka timaganyu tina ndi tina kuti ndipeze ya zovala, zakudya ndi lenti. Ndinasungako K20 000 yomwe ndidapeza kudzera muganyu yotsitsa katundu anthu  akamachoka kumsika  ku Lilongwe pomwe amayi adayamba bizinesi yophika zigege kuti tizisunga ndalama pang’onopang’ono,” adatero Kumbemba.

Anzake atatsekera sukulu, adatero Kumbemba, mayi ake adamuuza kuti apite kusukuluko kukasungitsa malo ndipo chifukwa ndalama yomwe adampatsa yoyendera idali yochepa, adaganiza zoyenda wapansi.

“Koma mwachisomo cha Mulungu ndinakumana ndi galimoto yomwe inandiimira nditayenda mtunda ndithu. Anandinyamula kukandisiya ku Dedza. Pa roadblock ndinapempha chithandizo,” iye adatero.

Kumbemba adati akuthokoza a Chibambo, a Kampanikiza komanso onse omwe amuthandiza ndipo walonjeza kuti akalimbikira sukulu kuti adzathandizenso ena mtsogolo.

Iye adati nkhani zomwe zikumveka zoti amamwa mowa ndipo makolo ake adamunyanyala kumulipilira fizi ndi zabodza.

Mayi a m’nyamatayu a Caroline Lipenga adauza Msangulutso kuti Kumbemba ndi woyamba kubadwa pa ana atatu ndipo amakhala ndi bambo ake omupeza.

A Lipenga adati mwanayu wakhala akuthandizidwa ndi abambo ake omupezawa omwe amaphunzitsa pa Chitundu CDSS komanso amalume ake omwe ali m’dziko la South Africa.

“Mwana wangayu adakayamba sukulu ku Chanco mwezi wa May koma adasiya atangophunzirapo kwa sabata zingapo chifukwa cha mavuto a za chuma,” iwo adalongosola motero.

Iwo adati adampatsa Kumbemba K8 000 kuti ayendere popita ku Zomba koma idali yosakwana.

Si Kumbemba yekha yemwe akuvutika chonchi kuti aphunzire. Achinyamata ambiri maphunziro awo akuthera panjira kaamba kosowa fizi.

Izi zikuchititsanso kuti atsikana ena azichita mchitidwe woyendayenda posaka ndalama zoti alipilire maphunziro awo, apezere chakudya komanso pogona.

Malinga ndi mtsogoleri wa ophunzira pa sukulu ya ukachenjede ya University of Malawi a Charles Dokera, ophunzira ambiri akusiyira panjira sukulu chifukwa chosowa malo ogona komanso chakudya.

Iwo adati ena mwa ophunzirawo akumapeza mwayi wa ngongole ya sukulu fizi koma akumakanika kupeza chakudya ndi pogona.

Iye adati ophunzira 11 asiyiratu maphunziro awo pomwe ophunzira 403 ndiwo adali pa mavuto ndipo amafuna kusiya sukulu.

“Koma ophunzira anzawo tidalowererapo ndi kupeza njira zosonkhera limodzilimodzi,” adalongosola Dokera.

Related Articles

Back to top button