Kusamvana pa mwambo wokumbukira Chilima
Mwambo wokumbukira yemwe adali mtsogoleri wakale wa dziko lino a Saulos Chilima uchitika Lachiwiri likudzali kwawo ku Nsipe komwe thupi lawo lidayikidwa ngakhale kuti boma limafuna kuti mwambowo ukachitikire ku nkhalango ya Viphya, pa Phiri la Nthungwa komwe iwo adafera.
A Chilima ndi anthu ena 8 adamwalira pa ngozi ya ndege yomwe idachitika pa 10 June chaka chatha ku nkhalangoyo pomwe adali paulendo wokaika maliro a yemwe adakhalapo nduna ya za malamulo a Ralph Kasambala.

Koma pomwe boma lidali ndi lingaliro loti lidzachite mwambo wokumbukira za ngoziyo patatha chaka ku nkhalangoyo, a ku banja la a Chilima adanena kuti adakonza kale mwambo womwewo kwawo ku Nsipe.
“A boma adatiuza kuti ali ndi malingaliro odzapanga mwambo wokumbukira a Chilima ku Nthungwa, koma tawauza kuti ngati banja takhala tikukonza mwambowo kwa miyezi itatu ndiye sitingasinthe mapulani athu ayi,” adatero woimirira banja la a Chilima a Ben Chilima.
Iwo adatsindika kuti a banja sakuletsa boma kukonza mwambo ulionse ayi ngati ali ndi chikonzero chotero ndipo kuti mamembala a banjalo omwe amakhala ku mpoto akhoza kudzapanga nawo mwambo wa boma atafuna kutero.
Koma mneneri wa boma yemwenso ndi nduna ya zofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu adati boma lakhala likufunsa maganizo kwa mbali zosiyanasiyana kuphatikizapo a banjawo komanso azipembedzo pa nkhaniyo.
“Tikamaliza kukonzekera, tidzalengeza za mwambowo koma cholinga chathu nchoti mwambo wokumbukira anthu omwe adatisiya pangoziyo limodzi ndi a Chilima adzakumbukiridwe mwa ulemu ndi anthu onse,” adatero a Kunkuyu.
Mpakana pano, bomalo silidatulutse uthenga uliwonse okhudza mwambowo kuti Amalawi akhale n’chithunzithunzi cha chomwe chikuchitika ndi kutha kusankha komwe angadzalowere kukakhala nawo pa mwambowo.
Chipani cha UTM chomwe adayambitsa ndi malemu Chilima ndipo adali mtsogoleri wake kufikira tsiku la ngoziyo chanenetsa kuti chidzalondola komwe a banja adzapangire mwambo wawo.
A boma ndi a banja la a Chilima adakumana sabata yatha kukambirana za mwambowo komwe adalephera kumanga mfundo imodzi pa za mwambo koma a banja adaloleza boma kumangira a Chilima chiliza cha chikumbutso.
“Pa zokambirana zathu padatulukanso nkhani yokhudza kumanga chiliza cha chikumbutso chomwe boma lidati likufuna kumanga ndipo tidawaloleza koma bola adzakambirane ndi akadaulo a zomangamanga a ku banja pa momwe chilizacho chidzamangidwire,” adatero a Chilima.
Kadaulo pa kayendetsedwe kabwino ka zinthu m’dziko a George Chaima adati mkumano wambali ziwirizo utatha kuti nzosadabwitsa kuti mbalizo zasiyana maganizo ngakhale sizimayenera kutero.
“Iyi ndiyo idali nthawi yabwino yosonyeza kuyendera limodzi, zomwe zachitikazi zikupereka chithunzithunzi cholakwika kunjako. Owona aziti ku Malawi kulibe umodzi ndi mgwirizano komanso n’zosokoneza anthu odzavota,” adatero a Chaima.
Ndege ya mtundu wa Malawi Defence Force Dornier 228 MAFT03 yomwe idanyamula a Chilima ndi anthu enawo idagwa m’nkhalango ya Nthungwa ndipo kuchoka apo, pakhala pali kukokanakokana pakati pa boma ndi chipani cha UTM.
Ngakhale mbali zina zakhala zikuonetsa kusemphana, a banja la a Chilima silidabwere poyera kudzudzula boma ndipo m’zochitika zake zina limakhala ndi boma monga pokhazikitsa bungwe la chifundo la Saulos Klaus Chilima Foundation pa 13 February 2025.



