Kuunika za Simatimatiki
Mtsutso wabuka pakati pa zipani zotsutsa boma ndi bungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) pa nkhani yogwiritsa ntchito Simatimatiki.
Simatimatiki, malingana ndi wapampando wa bungwe la MEC a Annabel Mtalimanja, ndi dongosolo logwiritsa ntchito makina a makono polemba ovota m’kaundula wa zisankho komanso potumiza zotsatira.
Simatimatiki ndi chidule cha mawu a Chingerezi otchedwa Smartmatic Election Management System (EMS).
Zipani zotsutsa boma sizikufuna kuti Simatimatiki idzagwire ntchito pa zisankho za pa 16 Sepitembala poganiza kuti ena atha kudzatengerapo mwayi wobera zisankhozo.

Mlembi wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) a Peter Mukhito apempha kuti mndandanda wa maina ovota uwunikidwenso kaamba koti Simatimatiki idagwiritsidwa ntchito, komanso dongosololi lisadzagwire ntchito potumiza zotsatira za zisankhozo.
DPP ndi zipani zina zitatu zidapereka kale ku MEC magawo a Simatimatiki omwe akufuna kuti awaunike, koma mneneri wa MEC a Sangwani Mwafulira akuti bungwe lawo lakana pempholo..
MEC idaganiza zosintha dongosolo lolembetsera maina m’kaundula wa zisankho ndi kutumiza zotsatira zake atakaona momwe dziko la South Africa ndi Zambia adayendetsera zisankho zawo pogwiritsira ntchito Simatimatiki.
Kuchokera nthawi imeneyo, MEC yakhala ikukambirana ndi zipani za ndale ndi mabungwe moti nthumwi zina zidapita ku Zambia kukaphunzira za Simatimatiki.
Onse atagwirizana, MEC idagula makina 6 500 olembetsera maina m’kaundula ndi kutumizira zotsatira za zisankho.
Atafika makinawo pa bwalo la ndege la Kamuzu International Airpot, akuluakulu a zipani za ndale ndi mabungwe adaitanidwa kuti akachitire umboni.
Mwadzidzidzi, MEC idadabwa kuti akuluakulu a zipani za ndalezo asintha maganizo awo zomwe katswiri wina wa za malamulo, yemwe sadafune kuti dzina lake litchulidwe, adati n’kulakwa chifukwa onse akhala akuyendera limodzi mpaka kudzafika pogula makinawo.
Wapampando wa bungwe la Civil Society Elections Integrity Forum a Benedicto Kondowe adati kusintha kwa dongosolo lolembetsera ndi kutumizira zotsatira za zisankho kutha kuonongetsa dziko lino ndalama zambiri.
Mmbuyomu a Mtalimanja adauza dziko lino kuti ndalama zoyendetsera zisankho zaperewera ndi K97.9 biliyoni.
Malingana ndi mkuluyu, MEC idapempha K220 biliyoni yoti iyendetsere zisankho za pa 16 Sepitembala.
“Mmalo mouza MEC kuti isagwiritse ntchito Simatimatiki zipani zotsutsa boma zingokambirana ndi MEC ndi cholinga chofuna kuchotsa nkhawa zawo,” atero a Kondowe.
Zipani zotsutsa zikuti m’maiko omwe adagwiritsa Simatimatiki pa zisankho monga Kenya, Venezuela ndi Phillipines zotsatira zake zidali zosadalirika, koma a Mtalimanja akuti izi ndi nkhambakamwa chabe.
MEC ikuti igwiritsabe ntchito Simatimatiki, koma nazo zipani zotsutsa zatemetsa nkhwangwa pa mwala kuti sizitheka.