Apolisi akonzeka kuthanandi ziwawa zokhudza ndale
KANDANI NGWIRA ndi BRIGHT KUMWENDA
Apolisi akuti apereka chitetezo chokwanira m’misonkhano yokopa anthu, povota komanso potulutsa zotsatira za chisankho cha pa 16 Sepitembala.
Mkulu wa polisi a Merlyne Yolamu ndiwo adalankhula izi pa msonkhano omwe bungwe la Public Affairs Committee (PAC) lidachititsa posachedwapa mu mzinda wa Blantyre.
“Tamva madandaulo a Amalawi okhudza ziwawa ndipo ndikufuna ndikutsimikizireni kuti tikuchita zotheka kuti tikhale ndi zisankho za mtendere,” iwo adatero.

Pothirirapo ndemanga, mkulu wa bungwe la Centre for Democracy and Economic Development (CDEDI) a Silvester Namiwa ndi wa Human Rights Defenders Coalition (HRDC) a Gift Trapence adadzudzula apolisi kuti akulekerera ziwawa za ndale.
“Ife tikuona kuti apolisi athu akulekerera ziwawa chifukwa sakumanga anthu omwe adachita za mtopola ku Mponela ndi ku Ndirande ngakhale anthuwo ali odziwika,” adatero a Trapence.
A Mary Navicha, a chipani cha Democratic Progressive Party (DPP), adagwirizana ndi a Namiwa komanso a Trapence.
“Mpaka pano apolisi sadagwirebe anthu omwe adaphwetsa matayala a galimoto za aphungu a Nyumba ya Malamulo,” iwo adatero.
Posachedwapa anthu osadziwika adavulitsa amayi nsalu za makaka a Malawi Congress Party (MCP) ndi kuwatsitsa m’minibasi ku Ndirande mu mzinda wa Blantyre pamene ku Mponela m’boma la Dowa anthu ena adaotcha minibasi ya chipani cha DPP.
Poyankha, a Yolamu adati apolisi amatengerapo kanthawi pang’ono kumanga anthu omwe akuwaganizira kuti apalamula mlandu ndi cholinga choti apeze umboni wogwirika.
Ngakhale ziwawa zikupitirira, mkulu wa polisi watsimikizira Amalawi kuti asade nkhawa popeza akonzekera mokwanira kuthana ndi mpungwepungwe uliwonse womwe ungadze pa nthawi ya zisankho.
A Yolamu adaonjezera kuti akhala akukumana ndi akuluakulu a zipani, a mabungwe ndi a mipingo n’cholinga chopeza njira zothetsera ziwawa za ndale.
Mkulu wa Oxfam a Lingalireni Mihowa adatsimikiza kuti bungwe lawo lakhala likukumana ndi apolisi n’cholinga chofuna kupeza njira zothana ndi ziwawa za ndale m’dziko muno.
Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe la Federation of Persons with Disabilities in Malawi (FEDOMA) a Ethel Kachala adati ziwawa za ndale zichititsa kuti amayi ndi anthu aulumali asatenge nawo gawo pa ndale.
Bungwe la Nation Youth Council lidachenjeza zipani za ndale kuti zilekeretu m’chitidwe wogwiritsa ntchito achinyamata pa ziwawa za ndale.



