Tidakumana Bwanji
MMulungu amadalitsa anthu ake m’njira zodwabwitsa.
Samuel Yohane, Mulungu adamuyendera mu njira yapadera.
Mnyamatayu amaimba kwayala pa mpingo wa Nchalo Seventh-Day Adventist (SDA) m’boma la Chikwawa.
M’chaka cha 2023, mnzake woimba naye kwayala adafika ku mpingoko ndi m’bale, Faith Tsirani.
Atamuona, Samuel mtima udadumpha mpaka adapempha mnzakeyo kuti adzabwere ndi Faith kwawo, koma zidakanika.
Patapita nthawi Samuel adakumananso ndi Faith ku gulu loimba la achinyamata lotchedwa Nchalo Adventist Youth Choir.
Pozindikira kuti Faith ndi mfupa la fupa lake ndi mnofu wa mnofu wake, Samuel sadazengereze kumponyera mawu.
“Panatenga miyezi itatu Faith andivomere ndipo adanditengera kumudzi kwawo kwa Mfunde ku East Bank.

“Adandirandira ndi manja awiri ndipo ndinacheza bwino ndi abale ake, komanso apongozi anga,” adatero Samuel.
Mnyamatayu akuti kwawo kwa Faith kudali chiphwando.
“Tidadya nsima, mpunga ndikukhwasulira nyama ya nkhuku ndi nkhunda. Tidatsitsira ndi bota,” adatero Samuel.
Faith akuti sadayembekezere kuti anfakumane ndi Samuel ku kwayalako.
“Nditaona zomwe amachitira ndidadziwa kuti wagwa nane m’chikondi.
“Atandiponyera chichewa ndinamugubitsa mpaka kundidandaulira kuti ndimulore.
“Zitatheka adabwera kwathu ndipo aliyense adamulandira ndi chimwemwe ndi kumpatsa m’dalitso wawo,” iye adatero.
Faith akuti atapita kwa Samuel adalandiridwa ngati mfumukazi.
“Akwawo adaonetsa kuti amafunadi mkwenya ena amati mkamwini,” iye adatero.
Samuel adati mwa Faith amapezamo zofuna zake zonse.
“Kuda kokongola, kudekha, kukonda, kumvera ndi kufatsa pochita zinthu—zonsezi zilimo mwa Faith,” idatero njondayo.
Faith adati Samuel ndi mwamuna wa masomphenya.
“Ndidayamba kumva za mkuluyu ndisadamuthire diso chifukwa cha mbiri yake yabwino,” adatero Faith.
Awiriwa akupempha achinyamata kuti azipemphera kwambiri ndi kusala kudya amafunafuna mnzawo womanga naye banja.
Samuel ndi Faith adachita chinkhoswe cha m’nyumba pa 27 April 2025 kwa Mfunde ku Livunzu ndipo pa 7 December 2025 m’busa Yohane Grant adamangitsa ukwati wawo pa mpingo wa Nchalo SDA.
Perekaniperekani adachitikira ku Kukhala Motel m’boma la Chikwawa.
Samuel ali ndi zaka 31 ndipo amachokera kwa Sekeni 2 m’dera la mfumu Lundu m’boma la Chikwawa.
Faith ali ndi wa zaka 24 ndi wa pamudzi pa Mfunde m’dera la mfumu Makhuwira m’boma lomwelo.
Awiriwa amakhala ku Nchalo komwe Samuel amagwira ntchito ya uphunzitsi pa sukulu ya pulaimale ya Sekeni pamene Faith ndi wa bizinesi.



