Chichewa

Lambani wadza ndi Knock Out

Listen to this article

Dzina la Limbani Banda, yemwe masiku ano amadzitcha kuti Lambanie Dube si lachilendo kwa otsata zoimba ku Malawi. Iye adatchuka zedi mmbuyomu ndi nyimbo yake ya Chisoni Nkumatenda ngakhalenso Kulira kwa Kholo. KONDWANI KAMIYALA adacheza naye kuti amve za chimbale chake chatsopano. Adacheza motere:

Banda: Tithane ndi kupondelezana
Banda: Tithane ndi kupondelezana

 

Chimbalechi chaphulidwa liti?

Chimbale chatsopanochi, chotchedwa Knock Out chidatulutsidwa pa 22 October chaka chomwe chino. Ichi ndi chimbale changa cha nambala 11.

 

Knock out, ndiye kuti chiyani?

M’Chingerezi, ndikhoza kumalizitsa kuti Knock out oppression, inde kuthana ndi kuponderezana. Tikuyenera kuthana ndi nsanje ndi nkhanza komanso zoipa zonse.

 

Choyenera kuchita nchiyani?

Maganizo athu ayenera kusintha basi. Sitingatukuke ngati tikupita kusukulu ndi cholinga chodzalembedwa ntchito basi. Tiyenera kupita kusukulu ndi maganizo akuti tidzalembe ena ntchito patsogolo. Dziko likusintha ili. Kalelo munthu akakhala ndi galimoto zimakhala ngati ndiwolemera koma onani lero aliyense akudziwa kuti galimo n’chinthu choti chimafunika pamoyo wa munthu kukhala nacho.

 

Kodi m’chimbalechi muli nyimbo zingati ndipo zina mwa nyimbozo ndi ziti?

Muli nyimbo 13 ndipo zina mwa nyimbozo ndi Stuck on You, Living in the Jungle, Tikufuna Yesuyo komanso ndaimbanso nyimbo ya Chisoni Nkumatenda mwa njira ina.

 

Udajambula kuti?

Nyimbo zina zidajambulidwa ku Greener Arts Studios msewu wa Chileka ndi Tiya Chalamwendo komanso ku Ralph Records ku Namiyango. Izitu ndi nyimbo za chamba cha reggae momwe onditsata amadziwira.

 

Mawu kwa Amalawi ndi wotani?

Amalawi achilandira chimbalechi ndipo akusangalala nacho. Langa ndi pempho kuti apitirize kutigwira dzanja. Kungoyamikira kokha si kokwanira, akuyeneranso kumatigula zimbalezi.

Related Articles

Back to top button
Translate »