Jannah Theme License is not validated, Go to the theme options page to validate the license, You need a single license for each domain name.
Nkhani

Mabungwe akufuna lamulo loletsa ziponda ku ndale

Mabungwe okhudzidwa ndi kayendetsedwe ka zisankho ati lamulo loletsa kugawa zinthu kwa anthu ngati njira yowakopera pa ndale (ena amati ziponda kapena kwayu) liyambe kugwira ntchito kuti nawonso aone zophunzitsa anthu m’madera.

Izi zidatuluka pa mkumano wa mabungwe ndi onse okhudzidwa pa nkhani ya zisankho Electoral Stakeholders Reference Group on Political Parties (ESRG), omwe udachitikira mu mzinda wa Lilongwe Lachiwiri.

Woyendetsa ntchito za ESRG a Christopher Naphiyo omwe  mgululi amaimirira bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) adati mabungwe akufuna kudziwa pomwe angolowere akamapita kokaphunzitsa anthu m’madera.

A Tenthani: Ofesi siyidakhazikike

“Choyenera kudziwa n’choti lamuloli limaposa kungoletsa khalidwe la kwayu pa ndale ndiye tikuyenera kupanga changu kuti liyambe kugwira ntchito kenako tiuzane kuti kodi anthu tingawawuze zotani kuti alimvetsetse,” adatero a Naphiyo.

Koma mkulu wa ofesi ya kalembera wa zipani za ndale a Kizito Tenthani adati padakalipano n’kovuta kuti lamulolo lingagwire ntchito molondola poti ofesi yawo siyidakhazikike bwinobwino.

Iwo ati akadali mkati mokhazikitsa ofesiyo kuti ikhoza kukhala ofesi ya ndondomeko zake zoyenera kutsata komanso pakufunika kulumikizana bwino kuti tigwirizane momwe tikuonera kuti ofesiyo ingathandize bwanji.

“Tikusonkhanitsa magulu osiyanasiyana monga a mabungwe, a za malamulo, a za maphinziro, a ndale ndi ena onse okhudzidwa ndi lamulo limeneli kuti tipangire limodzi ndondomeko zoyendetsera lamulolo,” adatero a Tenthani.

Iwo adati china chomwe magulu osiyanasiyana akuyenera kudziwa za lamulolo n’choti silikukhudza nthawi ya zisankho yokha koma magawo osiyanasiyana a ndale chifukwa kukopa anthu kumayambira patali.

Mmbuyomo, malamulo amangoletsa kugawa zinthu kuphatikizapo makaka a chipani kuchoka nthawi yomwe kampeni yatsekedwa mpakana nyengo yonse yovota, kuwerengera mpakana kulengeza zotsatira za chisankho.

Ganizo lokhazikitsa lamulolo lidabwera polingalira kuti andale ena amadyera masuku pamutu pa Amalawi pogwiritsa ntchito umphawi wawo n’kumawapatsa zinthu mosinthanitsa ndi voti kenako zikayenda n’kuwathawa.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button