Front PageNkhani

Mankhwala akumabedwa bwanji m’zipatala?

Listen to this article

Zikuoneka kuti dziko lino latha nzeru pa nkhani zobedwa mankhwala m’zipatala.

Ngati njira yothandiza kuthetsa mchitidwewu, panakhazikitsidwa makomiti m’zipatala zonse za m’dziko lino.

Anthu akulira kubedwa kwa mankhwala

Makomiti amenewa amayenera kumatsatira mmene mankhwala amayendera mpaka kukafika kwa wodwala. Koma izi zikuoneka kuti sizikusintha kalikonse.

Mwachitsanzo, usiku wa Lachiwiri, apolisi m’boma la Ntcheu anamanga a Christopher Zimbiri kaamba kopezeka ndi mankhwala mopanda chilolezo. Mankhwalawa akuganiziridwa kuti anachokera m’zipatala za boma.

Malingana ndi mneneri wapolisi m’bomalo a Jacob Khembo, a Zimbiri a zaka 27 a m’mudzi wa Bula kwa mfumu Kwataine ku Ntcheu analephera kuyankha atafunsidwa komwe anakatenga mankhwalawo kapena kusonyeza chizindikiro choti anachita kugula.

Nkhaniyi ndi kadontho ka madzi chabe chifukwa pali malipoti ambiri osonyeza kuti mankhwala sakutetezedwa. Kodi vuto ndi chiyani poti owayang’anira alipo?

Mkulu wa bungwe la zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) a George Jobe anati njira yokhala ndi makomiti oyang’anira mankhwala m’zipatala inali yabwino.

Koma iwo anati vuto lomwe lilipo ndiloti anthu omwe amasankhidwa ambiri sadziwa chomwe ayenera kuchita.

“Anthu amenewa amangosankhidwa chifukwa ali ku malo ozungulira chipatalacho. Choncho akasankhidwa, amangowauza kuti ayambe kugwira ntchito yawo osawauza momwe ayenera kuchitira.

“Ndimayembekezera kuti anthu akasankhidwa, apite kaye kukaphunzira mmene ayenera kugwirira ntchito yawo. Apo bii, kubedwa kwa mankhwala sikusiya,” iwo anatero.

A Jobe anapitilira kunena kuti chinanso chimene chimaonjezera kuti mankhwala azibedwa ndi kusowa kwa zizindikiro za mankhwala a boma.

Iwo anati kudakakhala kuti mankhwala a m’zipatala za boma ali ndi zizindikiro, bwenzi anthu akuopa kumawagulitsa chisawawa.

“Chimene ndikufuna n’choti  padzikhala kusiyana pakati pa mankhwala a boma ndi ena kudzera mu chizindiro. Koma mmene zili panopo, utha kuba mankhwala a boma n’kumagulitsa pamsika anthu osadziwa,” iwo anatero.

Mabungwe komanso mafumu akhala akudandaula za kubedwa kwa mankhwala mzipatala. 

M’mbuyomu, mfumu Nsamala ya m’boma la Balaka inati anthu akumidzi akumauzidwa kuti azikagula mankhwala pamene mzipatala akumabedwa.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button