Nkhani

Akuti bizinesi yogulitsa mabomba ndiyotentha

Kunjakutu kukuchitika malonda osiyanasiyana. Ena akugulitsa mtedza, mbatatesi kapena nthochi bola apezepo phindu ngakhale lichepe.

Komatu pali anthu ena omwe amafuna phindu lalikulu. Anthu ena ku Mwanza anaipeza yogulitsa mabomba.

Malingana ndi mneneri wapolisi m’bomalo a Hope Kasakula, anthu awiri awagwira ndi bomba lomwe amapita nalo ku Blantyre kuti akatakate.

Anthuwa, omwe ndi a Andrew Gauti  Stephano a zaka 31 a m’mudzi wa Dickson ndi a Justin Lewis a zaka 30 a m’mudzi wa Kunenekude ndipo onse amachokera ku dera lamfumu Kanduku m’bomalo.

Iwo anagwidwa pa malo a chipikisheni (roadblock) pa Nkulumadzi pa msewu wopita ku Blantyre Lolemba.

“Pa tsikulo cha m’ma 11 koloko usiku, apolisi anaimitsa galimoto yopita ku Blantyre ndipo atachita chipikisheni, anapeza bomba.

“Nthawi yomweyo a Justin analumpha m’galimotoyo n’kuthawira kutchire koma apolisi anagwira a Stephano. Bombalo analibisa mu saka komanso a Justin anawagwira pambuyo pake,” anatero a Kasakula.

Iwo anapitiriza kunena kuti  anthuwo atafunsidwa, kunaululidwa kuti bombalo limakagulitsidwa pa mtengo wa K1.2 miliyoni.

Malingana ndi zomwe ananena, sikuti anthu amagula bombalo kuti akamphulitsire wina, koma chuma chili mkatimo.

Pali chikhulupiriro choti m’chidamo muli madzi otchedwa Amina omwe akufunidwa kwambiri.

Awiriwa akayankha mulandu wopezeka ndi chida mosavomerezeka, malingana ndi mneneri wapolisiyo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button