Chichewa

Mavuto osakata pa Wenela

Listen to this article

 

Tidakhala malo aja timakonda pa Wenela ndipo zidaonekeratu kuti zochita zikusowa. Kodi n’kumachitanji pomwe zinthu zikukwera mtengo tsiku ndi tsiku ngati palibe womanga mabuleki?

Musandiuze za Moya Pete chifukwa momwe ndidakuuzirani muja, palibe icho achita. Dziko lili pa auto pilot basi.

Nanga inu! Kusakaza nkhalango kwagundikaku mungati zinthu zikuyenda? Kodi nkhalango ndidaisiya kwathu kwa Kanduku lero ndingakaipeze pamene ootcha makala sakugona koma kusaka njira zothera mitengo kumeneko? Pamene nkhalango zikutha, Moya Pete akungoti asiya kugwirizana ndi awo ampalamatabwa, kuwaletsa kudula kesha ndi msetanyani? Nanga abale ake andale amene amatulutsa nkhuni, matabwa komanso mbande za mitengo akuwasiya bwanji?

Aliyense akudziwa kuti Mowe Pati ali m’gulumo. Mulinso uyu Mulibe wa galimoto zake. Nanga uja mbale wathu wosowa ya lendi m’tauni Shati Choyamba wa ku Lower Shire!

Onse akuwadziwa.

Nanganso bwanji osauza abale ake a Eisssshcom, inde anyamata oonetsetsa kuti kuzima kwa magetsi kukufalikira bwino, inde kampani yogulitsa mdima nawonso amakhapa mitengo ati akonze mapolo! Kodi mdima amagulitsa? Mukadzapeza munthu akugulitsa mdima, dziwani satana ali bwino. Inde, Dyabulosi akaona munthu wotere amavula chipewa n’kugwada ndi kunena kuti: “Dutsani amfumu. Inu ndi munthu wamkulu zedi, thambo la kumwamba ndi dziko lapansi zonse zilambira ufumu wanu. Kuguwa kwanu palibe angayerekeze kufikako.”

Abale anzanga, nanga tsiku ndi tsiku, munthu wopuma, wa umunthu wake, angamasangalale kunena kuti lero ndizimitsa kuwala kuti akuba atambalale? Munthu wokhala ndi umoyo wauzimu n’kumanyadira kuti timakanda tifera kumagetsi chifukwa cholephera ntchito?

Zamanyazi.

Chilichonse sichikuyenda.

Nanga Adona Hilida ndiye ali kuti? Kuthawa pano pa Wenela mopanda mantha, mayi uyu ali ndi mafunso akuti ayankhe.

Nanga mwaiwala kuti iyeyo ndiye adanena kuti: “Amene adaombera Yomphwi ndikuwadziwa. Ndipo awo adasolola makobidi nkundigawira ndi zawo. Wakudya nawo alibe mlandu.”

Zoti ameneyu ndiye ankatsogolera tonse ojiya, osolola ndi osenza pano pa Wenela? Kodi iyeyo ndi Abiti Patuma bola ndani?

Ndipo pomwe ndikukuuzani nkhaniyi, mbale wake Oswin Pitapo akuyembekezera kulandira udotolo wake. Ndangomva kale kuti atatsindika kuti palibe katakwe ngati iye posolola, sukulu yaukachenjede kuja kwa Chikanda ku Zomba Lachisanu imayembekezera kumupatsa udotolo wovuta. Ati iye ndi Doctor of Philosophy in Colossal Tax Payer Pilferage of Extraordinary Proportions. Dotolo wamkulu. Chifwamba. Tsinzinantole wamkulu. Wamtali zala wamkulu kuposa onse. Nyapala. Wandende. Kaidi…

Nanga ndatukwana?

“A Ndirande iyi! Machinjiri iyo! Lilongwe kwerani ka Starlet aka mukafika!” ndidakuwa.

Gwira bango! Upita ndi madzi!kutenga!

Related Articles

Back to top button
Translate »