Chichewa

Mbewu ya chimanga izigwirizana ndi dera

Ngakhale mbewu za makono zimabereka mochuluka ndipo zina zimacha msanga, akatswiri a zaulimi wa mbewu akuti mlimi amayenera asankhe mbewu yogwirizana ndi nyengo ya m’dera lake kuti akolole moyenera.

Malingana ndi wa zakafukufuku wa mbewu ku nthambi ya zaulimi m’dziko muno a Frank Kaulembe, mbewu za chimanga zidagawidwa m’magulu atatu kuti zizigwirizana ndi nyengo za m’dziko muno kuti ngakhale madera ali osiyanasiyana alimi azikolola zochuluka ndi kumapuindula nazo choncho akuyenera kupanga chisankho choyenera pamene akugula mbewu kuti asasemphanitse.

Sankhani mbewu yoyenera kuti mupindule

Mwachitsanzo, iye adati pali mbewu zocha msanga zimene zimatenga masiku a pakati pa 80 ndi 90 kuti ziche choncho ndi zoyenera kudera kumene kumalandira mvula yochepa kuti ikamadukiza zikhale zitacha.

“Mbewu zina ndi zapakatikati kutanthauza kuti sizifulumira kapena kuchedwa ndipo zimatenga masiku a pakati pa 120 kulekezera 130 kuti ziche zimene zimayenerananso ndi kudera kumene kumalandira mvula ya pakatikati kuti ichite bwino.

“Mbewu zina zimacha mochedwa kuyambira masiku 150 kumapita m’mwamba ndipo ndi zoyenera madera amene amalandira mvula yochuluka kuti zichite bwino,” adafotokoza motero.

Pothirirapo ndemanga pa nkhaniyi, mphunzitsi wa zaulangizi ku Lilongwe University of Agriculture and

Natural Resources (Luanar) Paul Fatch adati madera amene amalandira mvula yochepa ndipo amafunika mbewu yocha msanga ndi amene ali kotsika.

Fatch adaonjeza kuti madera amene amalandira mvula yochuluka ndi amene amapezeka ku mitunda kapena kuti kumapiri choncho alimi a m’madera oterewa ali ndi mwayi olima mbewu zochedwa kucha.

“Mbewu zochedwa kucha zimene zimayenerana ndi madera okwerawa zokolola zake zimakhala zochuluka chifukwa zimakhalitsa m’munda koma mlimi amene ali kudera lotsika akatengeka ndi kuchuluka kwa zokololazi ndi kubzala, mvula ilekeza zisadache choncho sangaphule kanthu koma chachikulu ndi kuvomereza basi.

“Chimodzimodzi mlimi akatenga mbewu ya ku dera lotsika ndikukabzala ku dera lokwera sichitanso bwino,” adafotokoza motero.

Kaulembe adati izi zimakhala chomwechi chifukwa mbewu yofuna mvula yochepa ikalandira mvula yambiri imapezeka yakhwima koma mvula ikugwabe ndipo zotsatira zake zokolola zambiri zimaonongekera m’munda momwemo.

Katswiriyu adaonjeza kuti mbewu yochedwa kucha ikalandira mvula yochepa imadzasowa madzi panthawi yomasula kapena kuti yopanga njere choncho zokolola zake zimatha kukhala mphwemphwa, za magweru kapena kungochuluka zitsononkho basi.

Iwo adati izi zili chomwechi chifukwa nthawi yomasula madzi amafunikira kwambiri.

Kaulembe adachenjeza alimi kuti aziwerenga masiku pa pepala la mbewu akapita kogula ndikulinganiza

mmene mvula imagwera m’dera lawo ndikuona ngati ingakachite bwino kuti azipanga chitsankho

choyenera.

“Ngati izi ndizovuta kapena kuti sangakwanitse kutero azifunsa alangizi a m’dera la kwawo kuti awaunikire bwino,” adatero katswiriyo.

Pozindikira kuti nyengo ya m’dera lawo ya ku Lunzu m’boma la Blantyre mvula sichedwa kusiya, mlimi wina Kaitane Shuga adapanga chiganizo chobzala mbewu yocha msanga ndipo adati izi zikumuthandiza.

“Kale ndimangoumilira mbewu zamakolo zimene zimafuna mvula yochuluka choncho zaka zambiri

ndimabwerako ku munda manjamanja koma chiyambireni kubzala mbewu yocha msanga ya kanyani

ndimakolola ndipo palibenso amene angandinamize kuti ndizilima mbewu zamakolo chifukwa

ndinathana ndi njala,” iye adatero.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button