Mdima siukukata
Mafumu ndi anthu awo m’madera osiyanasiyana m’dziko lino, ati kuima kwa gawo 9 ya ntchito za magetsi a kumidzi ya Marep kwachititsa kuti chiyembekezo chawo chotukuka chizilale.
Malinga ndi anthu amene atolankhani athu acheza nawo m’madera osiyanasiyana, izi zikudzetsa kulira basi.
Kusowa kwa magetsiku kukuchititsa kuti anthu a bizinesi kusowa pogwira pomwe akufuna kuchita bizinesi zawo.
A Andrew Lazalo omwe ali ndi golosale m’mudzi mwa Mphamba kwa T/A Kachamba ati amayembekezera kuti magetsiwo athandiza kuti akuze bizinesi yake.
“Ndi loto langa kuti magetsi atabwera ndikhoza kugula filiji kuti ndizigulitsa zakumwa zoziritsa kukhosi ngakhalenso mkaka,” adatero iwo.
Unduna wa za mphamvu, Marep 9 ikuyembekezeka kufikitsa magetsi m’madera 416 m’maboma 27 a dziko lino kupatula Likoma chifukwa lonselo kuli kale magetsi.
Nyakwawa Mphamba ya m’deralo idagwirizana ndi nzikayo ndipo idati kuchedwa kwa magetsiwa m’dera lake kukuchititsa kuti ntchito za maphunziro, za umoyo komanso bizinesi zilowe pansi.
“Chiyembekezo chathu n’choti magetsiwa akadabwera bwenzi achinyamata athu akuchita bizinesi monga yometa komanso yogulitsa nyimbo ndi mavidiyo kupyolera pa kompyuta,” iwo atero.
Malinga ndi Senior Chief Malanda a m’boma la Nkhata Bay, maso akadali ku njira kudikira magetsi amenewa. Iwo adati amayi akuyenda mitunda yaitali kuti apeze zigayo, zimene zikadasintha ndi kubwera kwa Marep 9.
“Ifetu tidapereka kale madera amene tikufuna magetsi adzabzalidwe. Ndipo tikuyembekeza kuti magetsi asintha dera lino kwambiri tsono kuchedwaku tikudabwa nako,” adatero iwo.
A T/A Salima ndi T/A Makanjira, onse a m’boma la Salima ati maso akhala ali kunjira kuyambira pomwe adalandira kalata yofotokoza kuti ntchitoyo iya mba mwezi wa December chaka chatha koma mpaka lero, kuli ziiii.
“Ngakhale madera ena magetsi adafika, sitikudziwa kuti ndi gawo liti la Marep. Pali dera lina mbali mwa Nyanja komwe mpaka pano tikudikira jeneleta,” adatero a Makanjira.
Koma zonse zili apo, mafumu aakulu m’maboma a Chikwawa ndi Nsanje ntchitoyi ikuyenda.
Senior Chief Chapananga m’boma la Chikwawa ndi a Senior Chief Chimombo m’boma la Nsanje polankhula nthawi zosiyana ndi mtolankhani wathu, anenetsa kuti kwawoko anthu akumwemwetera ndi chilinganizo cha Marep 9 chomwe ati kwawoko chikusonya.
A Chapananga anati: “Mapolo a magetsi adafika kuno ndipo ali ku Novu ndi ku Phwadzi. Anyamata akugwira ntchito tsiku ndi tsiku ndipo ndife okondwa kuti kuno kuwala.”
Pounikira za kuchedwa kwa ntchitoyi, wachiwiri kwa mkulu wa Marep a Francisco Chingoli adati: “Madera omwe akutsalira ndi a m’maboma a Mangochi, Ntchitsi, Ntcheu, Thyolo komanso Neno omwe akugwiridwa ndi kontilakitala mmodzi chifukwa nthambi yovomereza makontalakiti ya PPDA idawavomereza chifukwa kampaniyo idapereka mtengo womverera kuposa ena.”
Iwo ati mwa madera 416 amene amayembekezera kuwafikira, akwanitsa madera 180 okha.
Poyamba ntchitoyi imayenera kutha pofika pa 31 March koma ntchitoyi ikuyenda mwa pendapenda zimene zikuchititsa kuti Amalawi akhumate. n
Atolankhani otolera: Zondani Mbale, Haneeph Mussa, Lovemore Khomo, Martin Gela ndi Wisdom Chirombo