Chichewa

Mike Mkwate: Chilombo pakati pa Bullets

Listen to this article

 

Dzina la Mike Mkwate si lachilendonso m’dziko muno malinga ndi ntchito yomwe akuphika ku Nyasa Big Bullets. Wasewera magemu awiri mu TNM amene adayamba mpaka kumaliza ndipo magemuwo adasankhidwa kukhala ‘Man-Of-Match’. Kusewera kwake kukupatsa chidwi anthu ambiri. BOBBY KABANGO adacheza naye kuti amve zambiri za iye motere:

Mkwate kunyadira kachikho ka  man-of-the-match
Mkwate kunyadira kachikho ka
man-of-the-match

Zabwinobwino mnyamata?

Bhobho, amwene!

Kodi Mike Mkwate ndani?

Ineyo ndiye Mike Mkwate, mwana wa ku Balaka koma ndikukhala ku BCA Hill ndi makolo anga mumzinda wa Blantyre. Ndili ndi zaka 20, woyamba kubadwa mwa ana awiri.

Kusukulu udapitako?

Pang’ono, amwene, ndidayambira sukulu pa Bangwe pulaimale, ndamalizira pa Matindi fomu 4 koma sindidakhoze bwino moti chaka chamawa ndibwerezanso. Ndikufuna ndikhoze bwino chifukwa ndili ndi lingaliro lopanga kosi ya unamwino (Nursing). Ndimafuna nditamadzasewera mpira koma ndikugwiranso ntchito.

Mpira udayamba liti?

Ndidayamba ndili wamng’ono kupulaimale. Zenizeni zidaoneka ndili fomu 2 ndikusewera ku Surestream.

Udalingalira kuti udzasewera ku Bullets?

Ayi. Moti tsiku loyamba kusewerera Bullets ndidali ndi mantha, ndimati ndikaona masapota aja ndiye ulakwitsenso, eeh! Ndidali ndi mantha, komabe anzanga amandilimbikitsa ndipo lero zikutheka, mantha adandichoka.

Ndi kangati udasankhidwa ‘man-of-the-match’?

Ndasankhidwapo kawiri. Ku Bullets ndasewera magemu 6 muligi koma awiri okha ndi amene ndidayamba mpaka kumaliza moti awiriwo ndidasankhidwa kuti ndasewera bwino. Magemu enawo ndimachokera panja. Ndikusewera mu Wizards ndidasankhidwanso kukhala man-of the-match maulendo 7.

Ndiwe Msilamu, kodi namazani simakusokonezani maseweredwe?

Osati kwambiri koma munthu ndi munthu, ngati sunadye umamva njala ndiye zimandikhudza inde, koma osati kwambiri.

Ndi wosewera uti amakusangalatsa? Nanga timu?

Henry Kabichi ndiye amandisangalatsa. Timu ndi Wizards ndipo ndine sapota wa Wizards koma ntchito ndimagwira ku Bullets. Kuti tisewere ndi Wizards, palibe kupereka mwayi kwa Wizards chifukwa timakhala tayamba ntchito yathu. n

Related Articles

One Comment

  1. He is a boy with a bright future……koma fodya ndamene amaononga ma player athu.

Back to top button
Translate »