Nkhani

Ndikulemba anthu 200—a Mutharika

Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika adzudzula anthu omwe akuti amawanena m’masamba a mchezo kuti sadalingalire amayi posankha maudindo ena omwe adaulutsa Lamulungu lapitalo poti palibe ngakhale mayi mmodzi m’gulu la osankhidwawo.

A Mutharika adatulutsa ukaliwo Lachitatu polumbiritsa nduna zitatu, mlembi kuofesi ya Pulezidenti ndi nduna a Justin Saidi ndi achiwiri awo a Stuart Ligomeka ku nyumba ya boma ya Sanjika mumzinda wa Bantyre.

A Mutharika kugwirana chanza ndi a Chaponda atawalumbiritsathe event. | Archangel Tembo, Mana

Nduna zomwe zidalumbirazo ndi a Joseph Mwanamveka womwe ndi nduna yazachuma, a Alfred Gangata womwe ndi nduna yazamdziko komanso a George Chaponda womwe ndi nduna yowona zamaubale ndi mayiko ena.

A Mutharika adati zamkutu kuti anthu ena makamaka mabungwe oyima pawokha ayambe kuwadzudzula atangosankhapo anthu ochepa chabe pomwe pali mipando 200 yoti ayikemo anthu ndipo odzudzulawo sakudziwa kuti mmipandoyo ayikamo ndani.

“Anthu ena adangobadwa ndi mtima wofuna kudzudzula APM [Arthur Peter Mutharika] basi. Akuti sindidalingalire amayi posankha maudindo, amva kuti ndamaliza kusankhako? Kungozolowera kuloza anzawo zala basi,” adatero a Mutharika.

Iwo adati kupatula mabungwe omwe amapanga za amayi, mabungwe ena onse mulibe amayi mmaudindo akuluakulu koma mabungwewo sawona zimenezo poti ndimnyumba mwawo koma akufuna kuloza zala anzawo.

Komabe iwo, adayamikira nthambi zina monga a mabanki kuti zikuyesetsa kuyika amayi mmaudindo akuluakulu zomwe adati ndikhumbo la boma la DPP kuti amayi azikhala m’maudindo.

A Mutharika adapambana pachisankho chapa 16 September 2025 koma chisadachitike chisankhocho, gulu lamabungwe omenyera ufulu wa amayi “Women Manifesto” lidakhazikitsa ndondomeko zomwe mfundo ina kumenyera amayi ufulu wokhala mmaudindo.

Nkulu wa gululo Mayi Maggie Kathewera Banda adati cholinga chomenyera ufulu wa amayi okhala mmipando nkuti nawonso azitenga nawo gawo popanga ziganizo zoyendetsera boma komanso azikayimilira zofuna amayi.

“Chomwe tikufuna nchakuti amayi nawo azikhala mmipando ngati abambo chifukwa onse ngofanana ndipo ali kuthekera koyendetsa maofesi ndikupanga ziganizo zobweretsa chitukuko,” adatero a Kathewera Banda.

Kumwambo wolumbiritsa nduna ndi alembiwo, a Mutharika adachenjeza ogwira ntchito m’boma kuti sadzasekelera mchitidwe uliwonse wa ulesi kapena osokoneza mapulani a boma.

Adachenjezanso ogwira ntchito m’bomawo kuti achepetse mikumano ngati pali mwayi woti akhoza kukambirana nkhani yomwe ilipo pa lamya kapena kudzera pa internet.

“Malawi ndi dziko la mikumano kwambiri, koma tiyeni tichepetse zokumana maso ndi maso nthawi zonse. Pomwe tingathe kukambirana pa lamya kapena pa internet tiyeni titero kuti tichepetse ndalama zotuluka,” adatero a Mutharika.

Kupatula a Chaponda, a Gangata a Mwanamveka, a Saidi ndi a Ligomeka, a Mutharika adasankhanso Lieutenant General George Alexander Jafu ngati mkulu wa asilikali ankhondo, a Kiswell Dakamau ngati oyang’anira nyumba zaboma, a Richard Chakupaleza Chikoko Luhanga ngati mkulu wapolisi ndi achiwiri awo a Stain Bamusi Chaima ndi a Mlowoka Noel Kaira.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button