Chichewa

Nkhawa akafuna kudzathandiza

Listen to this article

 

Ngati satenga madzi kunyumba, amavutika akafuna kuchita chimbudzi chifukwa kumalo awo antchito kulibe madzi.

Ichi ndi chibalo chomwe ogwira ntchito kunthambi yosunga katundu wa boma ku Blantyre, Central Government Stores, akuchita chifukwa bungwe la Blantyre Water Board (BWB) lidadula madzi mu March chaka chino. Apa n’kuti madziwo atangotuluka mu January ndi February kuchokera pamene adadulidwa zaka zitatu zapitazo.

Mmodzi mwa ogwira ntchito paofesiyo yemwe adakana kutchulidwa dzina adati atopa kutenga madzi m’makomo mwawo kukagwiritsa ntchito kuchimbudzi.

Mabikiri a madzi akumachoka kunyumba

“Ena sakubwera kuntchito chifukwa cha vutoli ndipo tipita kutchuti n’kudzabwera akayamba. Munthu ngati satenga madzi amadzipana kapena kukalipira ku Wenela. Palibe kuchitira mwina chifukwa zimbudzi ndi zamadzi, si zokumba,” iye adatero.

Wogwira ntchito wina adati ukhondo ukulephereka ndipo miyoyo ili pachiopsezo kaamba koti madzi omwe amabweretsa anthu sakwanira.

Patsikulo, zidadziwikiratu kuti pamalowa nkhani yodzithandiza ku chimbudzi ndi yovuta. Pomwe mtolankhaniyu amatengeredwa kuchipinda chosungira mbendera, amayi ena amachenjezana zosamala madzi adabweretsa ponena kuti ndi wochepa ndipo udali uli 10 koloko m’mawa.

Mtolankhaniyu atapempha malo okazithandizira adalowetsedwa mu chimbudzi cha amayi chomwe adati ndi cha ukhondo kaamba koti amabweretsa madzi tsiku lililonse.

“[Monga kasitomala] Asakaone nyasi ku chimbudzi cha abambo chifukwa sasamalako. [Abambo] kufooka kutenga madzi kuzisokoneza chisamaliro cha amuna ogula katundu,” adatero mayi wina.

M’chimbudzimu mudali bigiri ya madzi ndi mwaukhondo, koma ntchentche zikuwetedwa gawo la abambo komwe nyansi zikudzadza mtondo wa chimbudzi.

Mu zaka ziwirizo, anthuwa amagwiritsa ntchito zimbudzi za bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) komwe adawaletsa chifukwa amachulukitsa ndalama yolipirira madzi ku BWB pa mwezi.

“Ngakhale adatiletsa, m’mimba mukawira timakangocheza ku MEC komweko. Vutoli likusokoneza madongosolo achuma chathu chifukwa kupatula kudya tikufunika ndalama ya chimbudzi,” adatero bambo wina.

Pothirira ndemanga pankhaniyi, mneneri wa BWB, Priscilla Mateyu adati vuto ofesiyi siyimalipira ndalama yogwiritsira ntchito madzi.

Iye adati sanganene ndalama zomwe CGS ikuyenera kupereka ngati njira yolemekeza ufulu wa kasitomalayu.

Naye mneneri ku nthambi ya chuma cha boma, Alfred Kutengule, adati zangovuta kagwiritsidwe ntchito ka ndalama ku CGS, koma amalandira ndalama ngakhale zolipirira madzi.

“Ofunika kuyankhula ndi likulu la ofesiyi chifukwa nthambiyi ili ndi thumba lawo la ndalama,” adatero Kutengule. n

Related Articles

Back to top button
Translate »