Chichewa

Nkhondo ilipo mu afcon

Listen to this article
Atusaye (kumanja) kuthambitsana ndi mnyamata wa Ethiopia
Atusaye (kumanja) kuthambitsana ndi mnyamata wa Ethiopia

Kuphedwa kwa Ethiopia Lachitatu pa Kamuzu Stadium ndi Malawi komanso kuphedwa kwa Mali tsiku lomwelo ndi Algeria zikusonyeza kuti m’gulu B momwe muli matimu anayiwa mukhala ntchito yosayamba.

Tikukambamu timu iliyonse yasewera mipira iwiri, umodzi pakhomo ndi umodzi koyenda koma Algeria ndiyo yachita chamuna chifukwa yapambana onse.

Mali ndi Malawi ndiwo akusetekera pakamwa ngakhale sanadye mokwanira kutsatira kutolera mapointi atatu pamasewero awiri.

Mali idapha Malawi pakwawo 2-0 nkukagonja m’manja mwa Algeria 1-0 koyenda. Malawi idakwapula Ethiopia 3-2 nkugonja kwa Mali pamene Algeria yathambitsa Ethiopia 2-1 komanso Mali.

M’gululi ikutsogola ndi Algeria kutsatirana ndi Mali ngakhale ili ndi mapointi atatu chimodzimodzi Malawi koma iyo yachinyitsa chigoli chimodzi pamene Malawi yachinyitsa zigoli 4. Kumbuyo kuli Ethiopia yomwe sidatole pointi ngakhale imodzi.

Mumpikisano wa Afcon matimu awiri m’gulu lililonse amene achita bwino ndiwo amapitirira kukapikisana nawo. Apa zikusonyeza kuti masewero onse akatha woyamba ndi wachiwiri adzapita ku Morocco chaka chikubwerachi.

Mpikisanowu ukatha, timu imodzi yomwe yathera pa nambala 3 koma yasewera bwino kuposa matimu onse amene sadachite bwino idzasankhidwa kuti ipite nawo ku Morocco.

Nkhondo m’gulu B ikuoneka ikhala pakati pa Mali ndi Malawi kuti apitirire Algeria yomwe yathobola kale ngakhale Ethiopianso ili ndi mwayi wochita bwino.

Malawi pa 11 October ikulandira Algeria, timu yomwe adayigonjetsa 3-1 mu 2010. Masewerowa ali pa Kamuzu Stadium ndipo Lachitatu lake pa 15 Malawi idzatsatira Algeria m’dziko lawo kukaphana. Timu ya Algeria idakhalapo katswiri wa mpikisanowu mu 1990 itaphwasula Nigeria.

Kuti Malawi ichite bwino ikuyenera ithethetse Algeria pamene ikubwera pa Kamuzu Stadium komanso kudzapha Mali imene idzafike pa Kamuzu Stadium pa 15 November komanso iyesetse kutidzimula pakati pa Ethiopia kapena Algeria kwawo kapena pakavuta kukangolepherana nawo.

Padakalipano, timu iliyonse m’gululi ili ndi mwayi wopita ku Morocco ngati ingasamale ndi magemu akudzawa.

Masewero a Malawi ndi Ethiopia, adachinya zigoli za Malawi adali Atusaye Nyondo ziwiri ndi Frank Banda, pamene Ethiopia adayichinyira adali Getaneh Kebede ndi Yusuf Saleh.

Related Articles

Back to top button
Translate »