Nyumba isanthula uthenga wa APM
Aphungu a Nyumba ya Malamulo dzulo (Lachisanu) akwangula kusanthula uthenga omwe mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika adapereka potsegulira mkumano wa 52 wa nyumbayo.
A Mutharika adatsegulira mkumanowo pa 31 October 2025 kuti aphungu azukute theka la bajeti ya 2025/26 pambali pokambirana nkhani zina monga kuunika kuthekera kwa mkulu wapolisi yemwe a Mutharika adasankha.

Poyamba kuyankha uthenga wa a Mutharika mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma a Simplex Chithyola Banda omwenso amaimirira chipani cha MCP adati mbali yotsutsa izitsutsa zokhazo zofooka ndipo izipereka upangiri poyenera.
“Sikuti t izingotsutsa chifukwa ndi fe otsutsa ay i , t iziuniki ra pomwe p a k u l a kw i k a n d i p o t i z i p ereka magan i zo a momwe zinthu zikuyenera kuyendera ,” adatero a Chithyola Banda.
I w o a s a d a y a m b e ndemanga yawo pauthenga wa a Mutharika, adayamikira mtsogoleri wakale a Lazarus Ch a kwe r a c h i f u kwa chovomereza zotsatira za chisankho kuti m’dziko muno mukhale bata ndi mtendere.
“Zonse tikupanga panozi n’chifukwa choti ti li pa bata ndi mtendere ndipo izi z idatheka chifukwa cha kukoma mtima kwa a Chakwera. Sadalingalire za mpando ayi koma mtendere
pakati pa Amalawi,” adatero a Chithyola Banda.
Koma iwo adadzudzula b oma ku t i l i k u zu n z a a c h i n y ama t a o m w e a k u w a g a n i z i r a k u t i ada l i az i kwanje omwe amasokoneza ziwonetsero nthawi ya ulamuliro wa MCP.
Iw o l i m o d z i n d i mt sogoler i wa chipani cha UTM m’Nyumba ya Malamulo a Patricia Kaliati komanso mtsogoler i wa chipani cha PDP a Kondwani Nankhumwa adauniki ra magawo angapo muuthenga wa a Chakwera.
Mwa zina atsogoleriwo adayamikira ganizo lotsegula kampani ndi mafakitale komanso zofuna kukonza ntchito zamigodi, matumba a ngongole za amayi ndi achinyamata ndikukwenza ndalama za chitukuko za CDF.
“Zimenezi ndi mfundo zabwino koma mukuyenera k u o n e t s e t s a k u t i paikidwa ndondoomeko zoyenera zokwaniritsira masomphenya amenewa. Pakafunika gawo lathu, tizithandizira kuti limodzi titukule miyoyo ya a Malawi,” adatero a Chithyola Banda.
A N a n k h u m w a adaunikira boma la DPP kuti lizikumbukira kuti a Malawi adzawaweruza ndi ntchito zomwe awapangile pazaka zomwe akhale pa mpando.
“ N t h a w i p a l i b e mukuyenera kuyambapo n t c h i to m o nga mwa malonjezo anu, osatengeka ndi zomwe ena akunena kuti mwangolowa kumene m’boma, mudzazindikira nthawi itatha musadapange k a l i konse,” adatero a Nankhumwa.
Koma kupatula kuyankha uthenga wa a Mutharika, a Kaliati adati chipani cha UTM chikufuna boma la DPP lifufuzenso chomwe chidachititsa ngozi ya ndege yomwe idapha yemwe adali mtsogoleri wachipanicho a Saulos Chilima ndi anthu ena 8.
Iwo amatanthauza ngozi ya ndege ya asilikali yomwe i dagwera m’nkha lango ya Chikangawa ndipo a Kaliati adati malipoti onse omwe adatuluka okhudza ngoziyo samveka ku chipani cha UTM ndiye pakhale kafukufuku wina.
“Ti k u f u n a t i d z i w e munthu amene adauza a Chilima ndi anthu ena 8 kuti akwere ndege yomwe ankadziwa kuti idal ibe mafuta,” adatero a Kaliati.
Aphunguwo amal i za dzulo kusanthula uthenga wa a Muthar ika ndipo k u y ambi r a L o l emba api t i r iza kukambi rana nkha n i z i na ndi z i na kuyembekeza kuti nduna ya za chuma a Joseph Mwanamveka adzalengeze bajeti.



