Chichewa

‘Pewani chukwu Ku mtedza’

Chukwu kapena aflatoxin m’Chingerezi ndi liwu lomwe silichoka pakamwa ku ulimi wa mtedza m’dziko muno chifukwa ndi chipsinjo chachikulu ku ulimiwu.

Chukwu chikuchititsa kuti mbewuyi isamapeze mwayi wogulitsidwa m’misika yakunja komanso chikuika miyoyo ya anthu pachiopsezo cha matenda osiyanasiyana monga khansa.

Malingana ndi woona za kafukufuku wa mbewuyi ku nthambi ya zakafukufuku wa zaulimi wa mbewu m’dziko muno Donald Siyeni, nyengo yokumba, kuumitsa ndi kusunga mbewuyi ndi yofunika kwambiri kusamala chifukwa ndi imodzi mwa nyengo imene mtedza umachita chukwu kwambiri.

“Kawirikawiri, izi zimachitika ngati mlimi wakumba mtedza mofulumira kapena mochedwa, akamakhapa mtedza pokumba komanso ukakhala kuti sukupitidwa mpweya poyanika,” iye adatero.

Siyeni adati mtedza wosakhwima umakhala ndi madzi ambiri choncho umagwidwa ndi tizilombo toyambitsa chukwu mosavuta.

Kuonjezera apo, iye adati kuchedwetsa kukumba mtedza utakhwima kale kumakhala ngati kupereka mwayi kwa tizilombo toyambitsa chukwu timene timapezeka m’nthaka kuti tigwire mtedzawo.

Alimi ayenera kuyanika mtedza kuti uume bwino

Ngati njira imodzi yothandiza kudziwa ngati mtedza wakhwima ndipo mlimi akhoza kuyamba kukumba, mlangizi wa mbewu m’boma la Dowa, Sangayemwe Kausiwa adati choyambirira, mlimi azule maphata a mtedza mbali zonse za munda uja okwana 10.

Akachoka apo, iye adati athothole mtedzawo ndi kusakaniza.

“Pambuyo pake atape mtedza wokwana 100 ndi kuyamba kuswa ndipo akapeza kuti mtedza 70 kupita m’mwamba mkati mwa zikhokho zake mukuoneka madontho akuda, mtedza weniweniwo ukuoneka waukulu, wolimba komanso wabwera mtundu woyenera ndiye kuti wakhwima akhoza kuyamba kukumba,” adafotokoza motero.

Siyeni adati mlimi akakumba mtedza tsiku lomwelo asase dothi lonse ndi kuuyanika asadauthothole pozondotsa maphatawo ndi kuwayang’anitsa kumwamba kuti uzipitidwa mpweya okwanira.

Iye adati maphatawo ayenera kusanjidwa m’mizere osati kungounjika pamodzi ndipo mlimi athothole mtedzawo pakapita masiku atatu kapena 5.

“Mlimi ayanike mtedza umene wathotholawo kwa masiku ena atatu kapena 5 padzuwa ndipo akatero asankhemo mphwemphwa ndi onse oonongeka.

“Alimi ena amathotholeratu mtedza akakumba ndi kumauyanika choncho aonetsetse kuti akuyanika pamalo posafika chinyontho komanso auyanike mosachepera masiku 6,” adatero iye.

Mkuluyo adaonjeza kuti malo osungira mbewuyi ayenera akhale ouma komanso odutsa mpweya bwino chifukwa kupanda kutero umachita chukwu.

Iye adati chinthu china chimene alimi akuyenera kusamala ndi kuonetsetsa kuti pamene akuchotsa makoko mtedza wawo usamasweke ndipo asamagwiritse ntchito njira yonyika m’madzi chifukwa kutero ndi kuika mbewuyi pachiopsezo chochita chukwu.

Joseph Banda, mlimi wa mtedza m’boma la Lilongwe adati nthawi yokolola mtedza sachita nayo chibwana choncho amayesetsa kutsatira ulangizi wonse woyenera kuti akafike pamsika ndi mbewu yosiririka m’maonekedwe.

“Mtedza ukakhala wokhapikakhapika komanso ukakumana ndi chinyontho umaoneka wakuda. Zotsatira zake siuyenda malonda kapena umangogulitsa mongotaya,” adafotokoza motero.

Neston Maganizo, mlimi wina wa m’bomalo adathirirapo ndemanga kuti nthawi yokumba mtedza ndi kuumitsa ndi yofunika kwambiri ku ulimiwu ndipo kupanda kusamala umaphonyana ndi makwacha.

“Iyi ndi nthawi imene ife alimi a pagulu la Titukulane Cooperative timakhala tikukumana kwambiri ndi kumaphunzitsana kasamalidwe ka mbewuyi kuti ikafike kumsika ndi chikoka,” adaonjeza iye.

Kupatula nthawi yokolola, Siyeni adati mtedza umatha kugwidwa chukwu ukadali m’munda makamaka ngati nthawi imene ukubereka wakumana ndi ng’amba motsatizana ndi mvula yowaza.

Related Articles

Back to top button