Chichewa

‘Pewani ngozi, kuberedwa’

Listen to this article

Nyengo ya Khirisimasi ndi Nyuwere kumachuluka ngozi za pamsewu, mchitidwe wa umbava ndi umbanda komanso ngozi zina monga kumira m’madzi akusangalala.

Nthambi yoona za ngozi za pamsewu ya Directorate of Road Traffic and Safety Services (DRTSS) yakhala ikupereka malangizo kudzera m’nyuzipepala kuyambira pa December 14 2016 pofuna kuti anthu adziwe msanga za kapewedwe ka ngozi zisangalalo zisadafike pachimake.

Ngozi iyi idachitika sabata yangothayi

Nthambiyi yati kupatula zopangitsa ngozi zina, nkhani yaikulu imakhala kuyendetsa galimoto chiledzerere kapena galimoto zosayenera kuyenda pamsewu zomwe zimaononga miyoyo ndi katundu.

Chikalatacho chidatinso oyendetsa galimoto akuyenera kupereka mpata odutsa kwa anthu mmalo monse mowolokera ndipo asayankhule palamya akuyendetsa galimoto poopa kuti chidwi chawo chingathawire ku lamyako mmalo moyendetsa galimoto.

Nthambiyo idatinso okwera ali ndi udindo odziteteza popewa kukwera galimoto zomwe zadzadza kwambiri ndi kupewa kukakamiza oyendetsa kuti azithamanga ngati achedwa paulendo wawo.

Nawo apolisi ati anthu ali ndi udindo woteteza miyoyo ndi katundu wawo potsatira ndondomeko zomwe iwo amapereka chaka ndi chaka monga kuonetsetsa kuti asiya munthu okhwima maganizo pakhomo akamachoka.

Mneneri wa polisi James Kadadzera adati nthawi zambiri chifukwa chokomedwa, anthu amasiya pakhomo palibe aliyense n’kupita kokasangalala ndipo pobwera amapeza nyumba yathyoledwa.

“Njira ina nkuonetsetsa kuti pomwe ana akusewera kapena kusangalala, pali munthu wamkulu owayang’anira kuopa kuti angabedwe kapena kuvulala ngati ali okhaokha,” adatero Kadadzera.

Iye adatinso anthu omwe akuyenda kupita mmalo ataliatali kukasangalala monga kunyanja, akuyenera kuonetsetsa kuti akugona mmalo otetezeka bwino kuopa kupangidwa chiwembu monga kuberedwa kapena kuvulazidwa ndi kuphedwa kumene. n

Related Articles

Back to top button