Chichewa

Phindu lochuluka mu ng’ombe za nyama

Listen to this article

Ngakhale ulimi wa ng’ombe za nyama umafuna mpamba wochuluka komanso phindu lake limabwera mochedwa, akadaulo a zaulimi wa ziweto akuti ndi ulimi wolemeretsa kwambiri kusiyana ndi wa ziweto zazing’ono mlimi akautenga bwino.

Akadaulowa akuti mlimi amadya nazo bwino ng’ombe za nyama akamazikwatitsa ndi zachizungu ndi kuzinenepetsa asadazigulitse.

Malingana ndi mkulu woyang’anira ulimi wa ziweto m’boma la Kasungu Jacob Mwasinga, ng’ombe ya Malawi zebu kuikwatitsa ndi ya chizungu monga ya chi Brahman kapena Bosimala, ana obadwawo akamafika chaka chimodzi amakhala akula ndipo afika poti mlimi akhoza kupha pamene osakwatitsa amatenga zaka ziwiri.

Ng’ombe za Brahman zimakhala ndi nyama yochuluka

“Mlimi akazitsekera m’khola ng’ombezi kwa miyezi itatu ndi kumazidyetsera momwemo zakudya monga mapesi, zotsalira za mtedza osaiwala madeya, kuzipatsa mankhwala opha nyongolosi ndikuzitetezera ku nkhupakupa zimanenepa kwambiri choncho phindu lake limapambana.

“Mlimi akakwatitsa ng’ombe zake ndi zachizungu komanso kuzinenepetsa asadagulitse amakhala ngati wachepetsa nthawi yokolola komanso amadzichulukitsira zokolola ku ulimiwu choncho amapindula koposa,” iye adatero.

Mkulu woona za ulimi wa ziweto ku Shire Valley Agricultural Development Division (Shivadd) Dickson Mangadzuwa adafotokoza kuti kuzera mundondomeko yonenepetsa ng’ombe, mlimi amatha kuchulukitsa kulemera kwa ng’ombe yake ndi theka kupita m’mwamba pakutha pa miyezi itatu.

“Ndaonapo alimi akuonjezera makilogalamu 0.7 pa kilogalamu iliyonse ya ng’ombe yake kuzera mu ndondomekoyi choncho akagulitsa amapha nayo makwacha ochuluka chifukwa ng’ombe imagulitsidwa malingana ndi kulemera kwake,” adatero iye.

Iye adati kugula ng’ombe zazikulu kale ndi kumangozinenepetsa ndi kopindulitsa kwambiri chifukwa mlimi amangozinenepetsa kwa miyezi itatu yokha ndi kugulitsa choncho amapanga ndalama pafupipafupi ngati akuweta nyama zing’onozing’ono.

Mangadzuwa adafotokoza kuti iyi ndi njira yokhayo yothandiza alimi a ng’ombe za nyama kuti aziutenga ulimiwu ngati bizinesi.

Medison Semba wa m’boma la Blantyre ndi mmodzi mwa alimi amene amachita ulimi wonenepetsa ng’ombe za nyama ndikumagulitsa ndipo akuti ndi ulimi wopindulitsa.

“Kale ndimangoweta ndi kumagulitsa koma phindu lake silimakhala logwirika kufikira pamene ndidayamba bizinesi yomagula kwa alimi anzanga ndi kumazinenepetsa ndi kumagulitsa.

“Nthawi zambiri sindizinenepetsa kwa miyezi itatu chifukwa miyezi iwiri yokha zimakhala zafikapo poti ndikhoza kugulitsa. Ndikapyola miyezi iwiri anthu ogula amadadaula kuti nyama yachuluka mafuta chifukwa ndimapha ndi kumagulitsa ndekha,” iye adatero.

Malingana ndi mlimiyu, amadyetsera ng’ombe imodzi chakudya chokwana makilogalamu 8 patsiku.

Iye adafotokoza kuti chakudyachi chimakhala chakasakaniza monga madeya a chimanga ndi mpunga, udzu ndi mamolase.

“Udzu ndi umene umakhala wochuluka kwambiri pa zakudya zonsezi chifukwa ndi chakudya chodalirika kwambiri cha ng’ombe,” iye adatero.

Ngakhale izi zili chomwechi, mphunzitsi wa zaulimi wa ziweto ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) Jonathan Tanganyika adati ulimi wa ng’ombe za nyama m’dziko muno ukukumana ndi mavuto monga kusowa kwa malo komanso zipangizo zodyetsera.

Kuonjezera apo, iye adati matenda komanso misika yosowa ndondomeko yoyenera ndi ena mwa mavuto amene akulowetsa pansi ulimiwu m’dziko muno.

Related Articles

Back to top button
Translate »