Chichewa

Silungwe kufotokoza za lamulo la Covid-19

Listen to this article

Boma lakhazikitsa lamulo lomwe cholinga chake ndi kuteteza anthu m’dziko muno ku matenda a Covid-19. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi woimira boma pa milandu Chikosa Silungwe kuti afotokoze zambiri za lamuloli.

Tafotokozani, kodi lamulo lolimbana ndi Covid-19 likutanthauzanji?

Lamuloli monga mwanena kale cholinga chake n’kuthandiza boma, komanso anthu kulimbana ndi mlili wa Covid-19. Tanthauzo la lamuloli ndiloti tsopano boma lili ndi chida chomwe chikupatsa nthambi zake monga zachitetezo ndi zaumoyo mphamvu zoonetsetsa kuti munthu aliyense akutsatira ndondomeko zopewera matenda a Covid-19. Popanda lamulo zimakhala ngati aliyense ali ndi ufulu wotsatira ndondomekozo kapena ayi chifukwa padalibe chomupanikiza kutero. Tsopano aliyense kaya akufuna kaya sakufuna akuyenera kutsatira ndondomeko zodziteteza ku Covid-19.

Silungwe: Tiyeni tigwirane manja

Kodi mphamvu za lamuloli zagona pati?

Lamuloli lili ndi zilango zosiyanasiyana. Mwachisanzo, muli zindapusa za ndalama, kulandidwa ziphaso za bizinesi, komanso ena akhoza kuona ngati malodza akupita ku ndende kukakhalako mwina mpaka miyezi itatu chifukwa chonyozera lamuloli. Anthu adziwenso kuti nthambi zachitetezo zapatsidwa mphamvu zogwiritsa ntchito njira iliyonse yomwe akuona kuti ithandiza kuti anthu atsate zomwe lamuloli likunena ndiye pena pake anthu angadzaone ngati nkhanza, koma ndi mphamvu zochoka mu lamuloli.

 Kodi zindapusazo zikuchokera pati?

Lamulo likunena kuti munthu aliyense akuyenera kuvala masiki akakhala pagulu, kupanda kutero achitetezo akamupeza adzalipira ndalama zosaposera K10 000 kapena kukagwira ndende ya miyezi itatu. Lamulo likutinso munthu aliyense asakwere galimoto basi kapena minibasi osavala masiki, kupanda kutero mwini galimoto akuyenera kulipira ndalama zosaposera K100 000, kupita ku ndende kwa miyezi itatu, komanso zikhoza kukhala m’manja mwa achitetezo ndi boma kulanda chiphaso chake cha bizinesi. Lamulo likutinso misonkhano yagulu iyime kupatula yokambirana za Covid-19 moti kupezeka ena akukumana mozemba mwini malo womwe akukumaniranapowo akuyenera kulipira ndalama zosaposera K100 000, kupita ku ndende, komanso akuchita tsoka malo akewo akhoza kutsekedwa.

Mukukambakamba za misonkhano ya gulu, kodi mukati gulu mukutanthauzanji?

Malingana ndi lamuloli, gulu likuyambira pa anthu 10. Izi zikutanthauza kuti msonkhano wa anthu oposa 10 ndiwoletsedwa. Dziwani kuti izi zikukhudza msonkhano wa mtundu uliwonse kupatula womwe akukambirana za Covid-19, komanso maliro omwe lamulo likulola anthu 50 koma woti adziteteza mokwanira ndipo akutsatira ndondomeko zina monga kusamba m’manja ndi kukhala motalikana. Dziwani kuti maliro a munthu wazizindikiro za Covid-19 kapena womwalira ndi matendawa akuyenera kuika ndi azaumoyo okha basi. Zitsanzo za misonkhano yagulu yoletsedwa ndi zinkhoswe, maukwati, masewero, misangulutso ndi mapemphero omwe aposa anthu 10.

Nanga m’maofesi momwe muli anthu oposa 10?

Lamulo silidasiye gawo, lakhudzaponso zamagwiridwe antchito. Akuluakulu a malo wogwira ntchito akuyenera kuonetsetsa kuti antchito awo adziteteza mokwanira. Ngati pali ena oti atha kugwirira ntchito yawo kunyumba, anthu otere apapatsidwe mwayi kuti paofesi pakhale anthu ochepa. Kuonjezera apo, mwabwana ali ndi udindo odziwitsa azaumoyo antchito awo akamaonetsa zizindikiro za Covid-19 kuti apange zotheka kutengera anthuwo ku malo woyenera kuti anzawo asatengereko. Antchito nawo ali ndi udindo odziwitsa mabwana awo za anzawo omwe akusonyeza zizindikiro za Covid-19. Izitu zikuchitika pofuna kuteteza anthu ku mliliwu.

Ndiye pakumveka za m’bindikiro (lockdown), kodi zikukhala bwanji?

N’zoona lamuloli likupereka mphamvu kwa nduna wa zaumoyo kulamula kuti pakhale m’bindikiro (lockdown). Apapa zikutanthauza kuti ngati nduna yazaumoyo mothandizana maganizo ndi akadaulo ndi nthambi zina zokhudzidwa awona kuti nkhondoyi ikutivuta ndipo Covid-19 ipitirira kufala, akhoza kulamula kuti m’bindikiro uchitike kwa masiku omwe akufunika. Anthu asade nkhawa chifukwa lamulo likufotokoza momwe zingakhalire kutakhala m’bindikoro kuti anthu asavutike. Sikuti momwe lamulo layamba kugwira ntchitomu ndiye kuti m’bindikiro wayamba ayi, pokhapokha zinthu zitafika poyipitsitsa, nduna ikhoza kulamula kuti m’bindikiro uyambe monga mwa mphamvu zake zomwe zili mu lamuloli.

 Kodi mungawalangize zotani Amalawi?

Langizo langa ndilapafupi! Amalawi, lamuloli labwera ndipo siladziko lina, koma la Malawi ndiye tiyeni tiligwiritse ntchito. Zisatengere anzathu achitetezo kapena azaumoyo kutiyendera kuti tivale mamasiki kapena kuti tisambe m’manja ndi sopo. Pewani kusonkhana m’magulu oletsedwa kuti mudziteteze, komanso muteteze abale anu ndi anzanu. Covid-19 ilipo ndipo ikuonetsa ukali wake, pafikapa sipolira wina kuima pachulu n’kumavina kuti mukhulupirire zoti kuli Covid-19. Dziwani lamulo lanu, limvetseni ndipo ngati simukulipeza kapena simukulimvetsa, funsani amfumu, azaumoyo m’dera lanu kapena ofesi ya DC ndi akuluakulu ena m’dera lanu. Tikagwirana manja polimbana ndi Covid-19, tipambana ndipo tipulumutsa mtundu wa Amalawi.

Related Articles

Back to top button
Translate »