Chichewa

Thirani manyowa mwachangu

Woona za kafukufuku wa za nthaka ku nthambi ya zakafukufuku wa zaulimi ya Bvumbwe m’boma la Thyolo Peter Mfune akuti kuthira manyowa mwachangu m’munda n’kopindulitsa.

Iye adati kuthira manyowa mwachangu kumathandiza kuti alowerere bwino m’nthaka choncho mlimi akabzala mbewu pomera imapezana ndi chakudya chokwanira ndipo imakula mwa mphamvu ndi kubereka bwino.

Mfune adaonjeza kuti m’zaka zina mvula yoyambirira imatsogozana ndi ng’amba kotero mlimi akathira manyowa moyambirira dothi limakwanitsa kusunga chinyontho kwa nthawi yaitali.

“Zotsatira zake mbewuzo zimapirira kung’amba ndipo sizipserera,” adafotokoza motero.

Alimi ayenera kukonza manyowa msanga, mvula isanadze

Malingana ndi katswiri wa zaulimi wa mbewu ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) Vernon Kabambe, mbewu za m’munda mmene mwathiridwa manyowa zimakhala kwa sabata ziwiri osaonongeka kukachita ng’amba.

“Manyowa amasunga chinyontho komanso mbewu zimene zalimidwa pa dothi la manyowa zimakhala za mphamvu ndipo zimakula mwachangu,” adatero iye.

Kuonjezera pa izi, mlangizi wa mbewu wa m’chigawo cha zaulimikwaLobim’boma la Dedza adaonjeza kuti kuthira manyowa nthawi yabwino kumathandiza kupewa kuchulukitsa ntchito pamene mvula yagwa.

Iye adati kuthira manyowa ndi ntchito yaikulu chifukwa amafunika ochuluka kuti akwanire munda wonse choncho mlimi akachedwa zotsatira zake amangothira chigawo chochepa kwinako n’kusiya.

“Mvula ikagwa zochitika kumunda zimachuluka zotsatira zake kuthira manyowa kumasiyidwa kaye m’mbuyo choncho popewa izi ndi bwino kuthiriratu.

“Kwa alimi amene amathirabe manyowa osapsa kuthira mochedwa kumaika pachiopsezo mbewu zawo chifukwa amakaotcha mbewu zija,” adatero mlangiziyo.

Chifukwa choti Eneles Timothy wa ku Ntonda m’boma la Blantyre amadaliramanyowa pa ulimi wake, amayesetsa kukonza ndi kuthira manyowa m’munda mwake mwachangu.

Iye adati amatsatira bwino ulangizi wa manyowa kutengera ndi mmene adaphunzitsiridwa choncho amapindula nawo.

“Ndi zoonadi kukachita ng’amba mbewu zanga sizifota msanga.

“Ndimakwanitsa kukonza ndi kuthira manyowa m’munda wanga onse ndisanafike mwezi wa October choncho mvula yobzalira ikagwa sindipanikizika ndimangoona zobzala basi,” adafotokoza motero.

Malingana ndi Mfune, kathiridwe ka manyowa m’munda kamatengera kuchuluka kwa manyowa amene mlimi ali nawo.

Iye adafotokoza kuti ngati mlimi ali ndi manyowa ochuluka, azithira manyowa mu khwawa lonse kapena kuti pakati pa mizere iwiri ndipo awakwirire akamapanga mizere yatsopano yobzalamo mbewu m’chaka chimenecho.

Ngati manyowa ndi ochepa, iye adati mlimi ayambe wapanga mizere m’munda mwake ndi kukumba mapando obzalamo mbewu pamlingo woyenera ndipo akatero athire manyowa m’mapandomo.

“Mvula ikagwa mlimiyo amayenera adzabzale mbewu m’mapando momwe adathira manyowa,” adatero iye.

Mfune adaonjeza kuti kuchuluka kwa manyowa amene mlimi akuyenera kuthira m’munda kumatengera michere imene ili kale m’nthakamo choncho alimi amayenera kuyezetsa nthaka yawo.

Ngakhale izi zili chomwechi, iye adati matani a manyowa osachepera 2.5 amafunika kuthira pa hekitala imodzi. 

Related Articles

Back to top button