Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu
Gift Banda ndi mkazi wake Tisunge Mandala adakumana koyamba ali ku sukulu ya sekondale ya Chiradzulu komwe ankaphunzira.
Atatsiriza maphunziro awo aku sekondale, amakumanabe m’njira ndipo amacheza nkhani ziwiri zitatu.
“Tikakumana tinkangocheza m’mene anthu amachezera, koma padafika poti tayamba kukumana mowirikiza ndipo chidwi ndi chikondi chidayamba kuchuluka mpaka ubwenzi udayamba,” adatero Banda.
Iye adati adamufunsira Mandala atakopeka ndi kumvera kwake akamuitana kuti abwere azacheze.
“Komanso nkhani zomwe tinkakambirana tikakumana ndi zomwe zidandikopa kwambiri mtima,” adatero Banda.
Awiriwa adakhala pa chibwenzi zaka zitatu asadalowe m’banja.
Paubwenzi wawo adakumana ndi zokhoma zingapo monga kukaikiridwa ndi makolo awo omwe amaganiza kuti akungochita zachibwana ngakhale eni akewo amadziwa kuti chikondi chawo n’chozama komanso chili ndi tsogolo lowala.
Iwo akulangiza achinyamata omwe akufuna kupanga chiganizo chopeza wachikondi kuti azidekha, kukhala ndi nthawi yabwino yomudziwa wachikondi wawo ndipo asathamangire zogonana asadapange dongosolo lonse lofunika.
Awiriwa akuti akakumana ndi mavuto m’banja mwawo amagwada pansi n’kupemphera kuti Mulungu awathandize.
“Ngati mwamuna ndimapereka mpata kwa mkazi ngati mbali imodzi ya banja kuti nayenso azitha kupereka maganizo ake pa momwe tingagonjetsera mavuto omwe takumana nawo,” adatero bamboyo.
Banda amagwira ntchito youlutsa mawu ku wailesi ya Capital FM pamene Mandala ndi mphunzitsi pa sukulu ya pulaimale ya Bangwe CCAP.
Pakadali pano awiriwa akukhala ku Mthandizi ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre.
Banda amachokera m’mudzi mwa Chauwa, Mfumu Ndakwera, m’boma la Chikwawa pamene Mandala amachokera m’mudzi mwa Kabambe, Mfumu Likoswe, m’boma la Chiradzulu.