Zikhalidwe zikukhomerera amayi
Wapampando wa Engalaweni Women Group a Mervis Mvula akuti zikhalidwe, zikhulupiriro ndi umphawi ndizo zikulepheretsa amayi ambiri kulowa ndale.
A Mvula alankhula izi ku Mzimba kumene mabungwe a Oxfam ndi Women Legal Resource Centre (WOLREC) amakumana ndi amayi, achinyamata ndi anthu aulumali omwe akuimira pa maudindo aukhansala ndi uphungu wa Nyumba ya Malamulo chaka chino.

“Anthu ambiri m’chigawo chino cha kumpoto amakhulupirira kuti mwamuna ndiye ayenera kupatsidwa udindo osati wa mzimayi.
“Mwana wa mwamuna amamuveka mphamvu zolamulira amayi akuluakulu. Si chifukwa choti mwanayo ali ndi nzeru kapena luntha loposa amayi ayi, koma chifukwa choti adabadwa wa mwamuna. Chomuyenereza chimakhala chimenecho basi.
“Takula ndi zikhalidwe zimenezi n’chifukwa chake ntchito yozisintha ikutenga nthawi yaitali kwambiri,” adatero a Mvula.
Iwo adati amayi akakwatiwa amachoka kwawo n’kukakhala kwa mwamuna wawo.
“Akafuna kuima amayamba apempha kwa abale ake a mwamuna wake ndipo amamukumbutsa kuti ndi mlendo, mtengwa pamudzipo, choncho sangawalamulire.
“Akakakamira amamuuza kuti akaimire kwawo. Akapita kwawo, amakumana ndi zokhoma zina.
“Abale ake amamuuza kuti sangaimire chifukwa adachokapo kale pamudzipo ndipo kwawo ndi kwa mwamuna wake. Zikafika pamenepa, amayi amagwira njakata, kuzingwa kwa kalulu thengo likapsa,” adatero wapampandoyu.
A Mvula adati amayi ambiri akukumana ndi zokhoma zambiri.
“Ndalama zochitira kampeni amayi zimawavuta, m’misonkhano anthu amawatchula kuti mahule, ena amawadera komanso kuwanyoza kaamba koti ndi amayi. Mavuto a amayi ndiwosayamba,” iwo adatero.
A Mary Kasambala, mmodzi mwa akuluakulu a Rumphi Women Forum, akugwirizana ndi a Mvula.
“Miyambo, zikhulupiriro ndi zikhalidwe za makolo zikuphwanya ufulu wa amayi pa ndale,” adatero a Kasambala.
Iwo adalimbikitsa amayi kuti ngakhale akumane ndi zokhoma asabwerere mmbuyo.
Wapampando wa Mulanje Rural Women’s Assembly a Catherine Chimenya adati m’chigawo cha kummwera amayi amakhala kwawo choncho ali ndi ufulu woima pa zisankho mosavuta.
“Mavuto omwe akukumana nawo ndi kusowa chuma chochitira kampeni, komanso kunyozedwa m’misokhano ya kampeni,” iwo adatero.
Mabungwe a Oxfam ndi WOLREC akulimbikitsa amayi, achinyamata ndi anthu aulumali kuti azitenga gawo pa ndale.
“Tikuphunzitsa amayi, achinyamata ndi anthu aulumali kuti apeze luso ndi luntha lochitira ndale,” atero a Sarah Misanje, katswiri wa Oxfam woona zoti pasakhale kusiyana pa ntchito zomwe amayi ndi abambo amagwira.



