Chichewa

Ziweto zisasowe mtendere m’khola

Listen to this article

 

yengo ya mvula ino, ziweto monga ng’ombe, mbuzi, nkhosa ndi nkhumba zimasauka kaamba ka matope m’khola, zomwe zimachititsa kuti ziwetozi zizisowa mtendere.

Nthawi zambiri ziweto zomwe khola lake limadikha, zimakhala zofooka nthawi zonse poti zimalephera kupuma mokwanira kaamba kakuti zimagona choimirira chifukwa cha chidikhacho.

Ng’ombe sizingapeze mtendere m’khola ngati ili. Ngakhale mkakawo ungakome?
Ng’ombe sizingapeze mtendere m’khola ngati ili. Ngakhale mkakawo ungakome?

Mkulu woyang’anira za ulimi wa ziweto ndi kuchulukitsa ziwetozo, Dr Ben Chimera, wati mchitidwe ngati umenewu umabwezeretsa ulimi wa ziweto mmbuyo chifukwa nthawi zina ziweto zimatha kugwidwa ndi matenda.

Pocheza ndi Uchikumbe, Chimera adati zoterezi zimachititsanso kuti mmalo monenepa, chifukwa msipu wamera, ziweto zimayamba kunyentchera kaamba koti mmalo moti zizidya, zimakhalira kugona kubusa.

“Zimadabwitsa kuti mmalo moti ziweto zizinenepa poti msipu wamera, zikunyentchera. Chifukwa chake sichikhala china, ayi, usiku zimakhala kuti zachezera chiyimirire ndiye masana zimafuna kugona pamalo ouma mmalo momadya,” adatero Chimera.

Iye adati ulimi wabwino wa ziweto n’kutsatira zomwe amanena a zamalimidwe pakakonzedwe ka khola la ziweto komwe kamathandiza kuti nthawi zonse m’khola muzikhala mouma ndi mwaukhondo.

“Pali njira zosiyanasiyana koma njira yosaboola m’thumba ndi yomanga khola pamalo otsetsereka kuti madzi asamadekha m’khola. Ziweto zili ngati anthu, nazonso zimafuna malo abwino kuti zizitakasuka,” adatero Chimera.

Mkuluyu adati kwa alimi a ziweto monga mbuzi ndi nkhosa, khola labwino ndi lammwamba kuti ndowe zizigwera pansi komanso madzi asamakhale mkholamo.

Chimera adati mlimi akhoza kumanga khola labwino pogwiritsa ntchito mitengo, luzi ndi tsekera ngati palibe ndalama zokwanira kugulira zitsulo ndi malata koma chachikulu nchakuti m’kholamo muzikhala mouma.

“Apa mutha kuona chomwe timalimbikitsira kubzala mitengo m’munda ndi pakhomo chifukwa sungavutike kokapeza mitengo yomangira khola, kungofunika kugula pepala lofolerera, basi kwinaku n’kugwiritsa ntchito luzi,” adatero Chimera.

Malingana ndi chimera, ziweto zokhala m’khola laukhondo zimadya mosangalala ndipo mpovuta kugwidwa ndi matenda ndipo zimaonekera bweya bwake kusalala kuti ndi zaukhondo.

M’midzimu, alimi ambiri amangozika mitengo mozungulira n’kusunga khomo nkumaweteramo ziweto zawo koma katswiriyu adati njira yotere si yabwino makamaka m’nyengo ya mvula ngati ino.n

Related Articles

Back to top button