Chichewa

Akhumudwa ndi kutsika kwa nandolo

Listen to this article

 

Alimi a nandolo ena m’boma la Mulanje, ati ali ndi nkhawa ndi kutsika mtengo kwa nandolo modzidzimutsa pamsika zomwe zikukayikitsa alimiwo ngati apindule naye chaka chino.

Mmodzi mwa alimiwo, Henry Kapalasa, wa m’mudzi mwa Chabwera kwa T/A Mabuka m’bomalo, adati nandolo watsika mtengo kwambiri padakalipano zomwe alimi sadayembekezere kuti zingatero popeza malonda adayamba bwino m’madera ambiri.

Pamene ena akolola nandolo, wina akadali m’munda kuti aume bwino
Pamene ena akolola nandolo, wina akadali m’munda kuti aume bwino

Kapalasa, yemwe ndi gogo wa zilumika zoposa 90, adati chiyembekezo chake pa mbewuyo chayamba kumira m’madzi popeza lingaliro loti apeza makwacha a nkhaninkhani pakutha pamsikawo, ayamba kukayikitsa.

“Kuno alimi ambiri tapeza nandolo wochuluka koma tsopano tagwira njakata ndi momwe zilili pamsika popeza miyezi yapitayi nandolo tinkagulitsa pa mtengo wa K600 pa kilogalamu koma tsopano lero wafika pa K300 pa kilo. Kutsika kotereku sikunachitikepo nkale lonse,” adatero Kapalasa.

Iye akuganiza kuti mchitidwewu nkubera alimi omwe amadalira ulimi wokhawo pa chaka kuti apeze makwacha otukulira banja lake.

“Chaka chino chimanga sichinachite bwino kudera lino moti anthu ambiri tayamba kale kukumana ndi mavuto adzaoneni ndi kukwera kwa mtengo wa chimanga popeza thumba la chimanga cholemera makilogalamu 50 lafika kale pa K12 000. Maso athu adali nganganga pa nandolo kuti mwina tikagulitsa tipeza ndalama zogulira chimanga, koma pamenepa tasowa pogwira,” anadandaula iye.

Kapalasa akufunitsitsa boma likadalowererapo msanga ncholinga choti alimi apeze phindu lokwanira pa ulimiwo.

Gogoyo akuganiza kuti kupanga magulu zingathandize alimiwo kupeza phindu lamnanu pa ulimiwo.

Alimi ambiri m’boma la Mulanje adakolola nandolo wochuluka ndiponso wina adakali m’minda kulindira kuti awume moyenera.

Masiku apitawo mkulu wa bungwe la alimi a nandolo la Nandolo Association of Malawi Susan Chimbayo adapempha alimi kuti asagulitse msanga nandolo wawo, komanso kuti akonze magulu kuti azikagulitsa ku makampani kumene mtengo umakhalako bwino.

“Makampani amafuna nandolo ochuluka choncho alimi ayenera

Related Articles

Back to top button
Translate »