Chichewa

Kufumuka si kulakwa, olemekezeka!

Listen to this article

 

Nkhani ili mkamwamkamwa panopa ndi yoti nduna ya zaulimi, mthirira ndi chitukuko cha madzi, George Chaponda, kudzanso mkulu wa bungwe la Admarc, Foster Mulumbe, atule pansi maudindo awo kuti komiti yomwe Pulezidenti Peter Mutharika wakhazikitsa kuti ifufuze za nkhani ya chimanga chomwe boma lidagula kudziko la Zambia igwire bwino ntchito yake.

Chaponda wanenetsa kuti satula pansi udindo wake monga nduna. Nayenso Mulumbe wati sanenapo kanthu pankhaniyi. Chaponda wati sakuonapo chomwe adalakwa ngakhale kuti akukhudzidwa ndi nkhani yogula chimanga kuchokera kudziko la Zambia kuti chipulumutse anthu kunjala yomwe yagwa m’dziko muno.

Zomwe zikumveka n’zakuti pakukhala ngati padalowa chinyengo malinga ndi mmene malonda a chimangawo adayendera. Izi zili choncho chifukwa mmalo mongogula chimangacho motchipa ku Zambia Cooperative Federation (ZCF) ogulitsa chimanga ku Zambia, boma la Malawi, kudzera ku bungwe la Admarc, lidaganiza zogula chimangacho pamtengo wodula pogwiritsa ntchito kampani yomwe si ya boma la Zambia yotchedwa Kaloswe Commuter and Courier Limited ngati m’khalapakati.

Chifukwa chogwiritsa ntchito kampaniyo pogula chimanga chokwana matani 100 000, boma la Malawi lidasakaza ndalama zokwana K26 biliyoni zomwe lidakongola kubanki ya Eastern and Southern African and Development, lomwe limadziwikanso ngati PTA Bank.

Achikhala kuti adangogula chimangacho ku ZCF, boma likadagwiritsa ndalama zokwana pafupifupi K15 biliyoni basi. Izi zikutanthauza kuti boma la Malawi lidasakaza ndalama zokwana pafupifupi K9.5 biliyoni zapamwamba pogula chimangacho kudzera kukampani ya Kaloswe Commuter and Courier Limited. Ho, zichulukirenji ndalama!

Funso n’kumati: Padali chifukwa chanji chosankhira njira yogula chimanga pamtengo wokwera chomwechi pomwe njira idalipo yopezera chimangacho pamtengo wotsika? Apa mpamene pakhota nyani mchira, n’chifukwa chake Amalawi ambiri, kuphatikizapo a mabungwe osiyanasiyana akuganiza kuti pena pake payenera kuti padalowa chinyengo—wina ayenera kuti adanyambitapo kena kake!

Ndikukumbukira nthawi ina yake Joe Manduwa, yemwe adali wachiwiri kwa nduna ya zaulimi nthawi ya Bakili Muluzi, ankayankha mlandu—ndaiwala pang’ono kuti udali mlandu wanji poti ndi kale limene lija. Manduwa, mwa iye yekha, adatula pansi mpando wake wonona ponena kuti ankafuna kuti chilungamo chioneke bwinobwino pamlandu wake posatengera kuti wavala “ministerial jacket” (jekete ya uminisitala).

Mwina a Chaponda ndi a Mulumbe, akadatengerapo phunziro pa zomwe adachita Manduwa potula pansi udindo kuti zofufuza ziyende myaa popanda zokayikitsa kapena zopingapinga. Ngati ofufuzawo sawapeza kulakwa pa zomwe zidachitikazo, sindikukayika kuti Pulezidenti Mutharika adzawabwezera pantchito zawo zofufuzazo zikadzatha.

Tsono ngati akuona kuti sadalakwe china chilichonse, makosanawa akuoperanji kufumukapo kuti apereke mpata kwa ofufuza kuti agwire ntchito yawo bwinobwinio?

Ndangonenapo ine, ndafumukapo kaye! Zili kwa iwo kunditsatira. n

Related Articles

Back to top button
Translate »