Chichewa

Luanar ikhazikitsa magulu a alimi akafukufuku

Listen to this article

 

Nthambi ya zaulangizi pasukulu yaukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) sabata zapitazo idakhazikitsa magulu a alimi a kafukufuku.

Magulu a alimiwa akhazikitsidwa ndi cholinga chopereka mwayi kwa alimi kuti atengepo mbali pa kafukufuku kuti apeze mayankho a mavuto omwe akukumana nawo paulimi.

Kwa nthawi yaitali, alimi akhala akungolandira zotsatira za kafukufuku kuchokera kwa akatswiri a kafukufuku ndi alangizi. Izi zapangitsa kuti alimi azingolandira chilichonse kaya ndi chogwirizana ndi kudera kwawo kapena ayi kotero kukhazikitsidwa kwa maguluwa kuthandiza alimiwo kupeza mayankho a mavuto a ulimi m’madera awo.

Ntchitoyi ndi ya zaka zinayi ndipo ikuchitika kudzera mupulojeketi ya Best Bets III ndi chithandizo chochokera ku McKnight Foundation. Magulu a alimi akafukufukuwa akhazikitsidwa m’madera a zaulimi a Zombwe m’boma la Mzimba, Mkanakhoti ku Kasungu ndi Kandeu ku Ntcheu.

Ena mwa alimi otenga nawo gawo pa chilinganizochi
Ena mwa alimi otenga nawo gawo pa chilinganizochi

Malingana ndi yemwe akutsogolera ntchtitoyi, Daimon Kambewa, kwa nthawi yaitali alimi akhala akutengedwa ngati osadziwa chilichinse kotero akatswri akhala akupanga kafukufuku paokha ndi kumawauza alimi kuti atsatire zomwe apeza. Izi zachititsa alimi kumangotsatira zilizonse ndipo njira zina sizinathandize kutukula ulimi.

Kutengapo mbali pa kafukufuku kuthandiza alimi kukhala ndi luntha ndi chidwi choganiza ndi kupeza njira zomwe zingawathandize kuthetsa mavuto awo paulimi mogwirizana ndi madera awo.

“Kwanthawi yaitali akatswiri a zaulimi akhala akupanga kafukufuku wawo paokha ndi kumawauza alimi zoti achite ndipo izi zapangitsa alimi kumangodikira alangizi kuti abweretse njira zatsopano za ulimi. Ntchito yopanga kafukufuku limodzi ndi alimi ithandiza kulimbikitsa kudzidalira komanso kukhala ndi luntha, luso ndi chidwi chithetsa mavuto a ulimi paokha,” adatero Kambewa.

Gulu lililonse lili ndi anthu 22 ndipo anthuwo asankhidwa ndi anthu a m’madera awo potengera chidwi chawo poyesera luso lamakono paulimi. Membala aliyense wa gulu akhala ndi munda wa chionetsero koma azikumana ndi kumakambirana nagawana nzeru.

Alimiwa aziyenderana m’minda ya wina ndi mnzake kuti aziphunzitsana ndi kumalimbikitsana.

Ntchitoyi ikuyembekezeka kuthandiza alimi kukhala anthu oganiza mozama pofuna kuthetsa mavuto omwe akukumana nawo paulimi ndipo zichepetsa mchitidwe wodalira kapena kudikira alangizi kuti awauze njira zothetsera mavuto awo popeza alangizi alipo ochepa kuyerekeza ndi alimi.

Ngati muli ndi mafunso kapena ndemanga, lemberani kalata ku:

Related Articles

Back to top button
Translate »