Chichewa

Malamulo Khumi pa Wenela

Listen to this article

 

Tsikulo Moya Pete adadabwitsa tonse. Adafika kumalo otsegulira msonkhano wa ana aja amalimbana za ziii! chaka ndi chaka ati kunamizira kutukula Wenela atavala ovolosi yake phiii!

Mukudabwa? Nafenso tidadabwa zedi chifukwa tsikulo lidali Lachisanu.

“Kodi mesa adati tizivala miyado, nkhwende, nyanda ndi zina zotere, tsono izi za maovololo zadza ndi yani?” Abiti Patuma adafunsa.

Abale anzanga inetu palibe icho ndidatolapo.

“Zinthu zina zimaphweka kuyambitsa koma n’zovuta kumalizitsa. Uku n’kuponya sitepe imodzi kutsogolo, atatu kumbuyo,” adaonjeza.

Sindikudziwa kuti izi zovala ovololo wazitengera kuti Moya Pete.

“Dzulo ndachotsa uyu ndalemba uyo, dzulo ndachotsa uyu kwambiri ndalembanso wina.  Ine ndi mlembi kwambiri, ndinenso mchotsi. Ndikunena pano mankhwala apezeka, misewu yochuluka ndikonza, mukanena za nyanja kwambiri, ndikuyankhani zimene ndakhala ndikunena kwa zaka 126. Amene sakudziwa akakolope nyanja kwambiri,” adatero Moya Pete.

Adalankhula nthawi yaitali, mpaka enafe tidayamba kugona.

“Inu mumayesa kuti ndikambapo za lamulo lakuti Paparazzi azitha kupeza zinsinsi zanga mosavuta mwauponda kwambiri. Ndingadzilume ndekha chala? Ana oipa moyo kwambiri,” adapitiriza Moya Pete.

Adamwera madzi, ena adali kuliza mkonono.

“Ndipo mumayesa ndinena za amene amagula mafupa a anthu a chialubino! Ng’oooo! Imeneyo si nkhani kwambiri. Opezeka ndi mafupa sakumangidwa? Ndiye ndikumva zamkutu kwambiri mukuti ndizisainira kunyonga akupha anthuwa? Mumfune,” adabwekera.

Adacheukira uku ndi uko.

“Msewu wa Kunenekude tikonza; msewu wa Chenzi tala adutsa kuposa pa Dzaleka pamene adafika zaka 8 zapitazo. Ngati mumaganiza ndichotsa Mowe Pati chifukwa chobweretsa miyandamiyanda ya anyamata athu a Dizilo Petulo Palibe kuti ayambe kulondera pano pa Wenela mwauponda,” adalankhulabe.

Adalankhula kwa maola angapo.

“Zaka ndi zaka mumatitaira nthawi kunena zomwezomwezo. Manyazi ndi umunthu mudazitayira kuti?” adatero Abiti Patuma.

“Musataye nthawi kunena za ine mutopa chifukwa panopa ndikutuma mwana wanga womupeza akasaine zikalata zina za boma kwambiri. Mwaiwala malamulo khumi?” adafunsa Moya Pete.

Sindingawaiwale mavesi amene tidaphunzira kusukulu sande:

Ndine Moya Pete, amene ndidakuchotsani muukapolo wa Adona Hilida wothawa chithunzthunzi chawo. Musakhale nawo atsogoleri ena pano pa Wenela koma ine ndekha. Muzipachika chithunzi changa pamakoma a nyumba zanu. Mukhoza kugwiritsa dzina langa kuti mupatsidwe msanga kontirakiti. Muzisunga tsiku limene ine Moya Pete ndidabadwa ndi kulilemekeza. Musalemekeze makolo anu ngati ndi a Polisi Palibe kapena Male Chauvinist Pigs. Mukhoza kupha, kuchita chisembwere, kuba ndi kunamizira ena ngati mukufuna kundisangalatsa. Mukhoza kulandaa mkazi wa mwini ngati anyoza Dizilo Petulo Palibe.

Gwira bango iwe! Upita ndi madzi!!! n

Related Articles

Back to top button
Translate »