Nkhani

‘BAMBO ATHOTHA MWANA’

Listen to this article

Bambo wina  m’mudzi mwa Nchada kwa T/A Nthondo ku Ntchisi amulamula kuti alipe mkazi wake ndi mwana wake wamkazi wa zaka 17, chipepeso cha K2 000 aliyense chifukwa chomuganizira kuti ankafuna kugonana ndi mwanayo mwezi wathawu.

Zamvekanso kuti msungwanayo sakuoneka komwe ali kaamba koti bamboyo wamumasula kuti si mwana wakenso kaamba koti adakana kugonana naye.

Koma bamboyo wakana kuti izi ndi zoona ponena kuti abale a mkazi wake ndiwo akumupekera nkhaniyi pofuna kumuipitsira mbiri.

Mayi a mtsikanayu (omwe sitiwatchula pofuna kuti anthu asamuzindikire msungwanayu) atsimikiza za nkhaniyi ndipo ati mwana wawoyo adasowa mwezi watha pa 21 May koma ati pochoka adauza mnzake yemwe amacheza naye kuti bambo ake amuuza kuti achoke pankhomopo chifukwa amakana kuchita nawo zachisembwere.

Mayiyo wati mu March mwanayo adawadandaulirapo kuti bambo akewo amamupempha kuti azigonana nawo ndipo kuti adzamukwatira mtsogolo koma atafotokozera mchemwali wawo wamkulu adawawuza kuti nkhaniyo asaipupulumire.

Iye wati mwezi wa April msungwanayo adakadandauliranso mayi ake aakuluwo kuti bambowo adamulondola kubafa komwe amasamba n’kumuuza kuti agonane koma mwanayo adawaopseza kuti akuwa ngati satuluka kubafako.

“Ulendo wachiwiriwu udatiopsa ndipo tidakatula nkhaniyi kwa amfumu omwe adatiitanitsa kukakamba nkhani ndipo amuna anga adawalamula kuti apepese mwanayo komanso ineyo ndi K2 000 aliyense,” adatero mayi a msungwanayo.

Iye adati sakudziwa chomwe amafuna pamwanayo koma ambiri akuganiza kuti amafuna kupanga chizimba.

“Takhala m’banja kwa zaka 27 ndipo tili ndi ana anayi, atatu aamuna ndipo wamkazi ndi yekhayu. Panopa anali mu fomu 4 pasukulu ina kuno ndipo akaweruka amagulitsa mugolosale kumsika. Ngati sindiwasangalatsa akanangondiuza kuti akufuna akwatire mkazi wina. Mwanayo adakakhala chitsiru bwenzi akumagona naye ine osadziwa,” adatero mayiyo.

Mkulu wawo mayiyo adavomereza kuti mu April mwanayo adawapezadi kunyumba kwawo kuwadandaulira kuti bambo akewo adamutsatira kubafa akusamba ndi kumuuza kuti akalola kugona nawo athetsa banja ndi mayi ake kuti amukwatire.

“Ulendo woyamba atandiuza mayi ake ndimaona ngati zamasewera koma ulendo uwu ndidadziwa kuti nkhani yake inali yaikulu ndipo ndidawafotokozera mayi ake kuti tikadandaule kwa mfumu,” adatero mayiyo.

Mfumu Pitala Kang’oma yomwe idaweruza nkhaniyi, yatsimikiza kuti izi zidachitikadi ndipo mpaka pano msungwanayo sakuoneka m’mudzimo.

Iye wati nkhaniyi panopa ili m’manja mwa apolisi omwe akuthandiza kufufuza komwe kuli mtsikanayo.

Koma bamboyo adati ili ndi bodza lamkunkhuniza.

“Nkhani imeneyi ndinaimva koma sindikufuna kuyaluka n’chifukwa chake ndinangokhala chete. Ndikudziwa zonsezi zikuchokera kwawo kwa akazi anga chifukwa sitigwirizana nawo,” adatero mkuluyu pouza mtolankhani wa Msangulutso aamfunsa kuti amve mbali yake palamya.

Adatinso abale a mkazi wakewo amusemeranso chinyau china ponena kuti adatukwana apongozi ake.

Apolisi ku Ntchisiko akuti afufuze kaye za nkhaniyi asanaperekepo ndemanga iliyonse..

Related Articles

Back to top button