Nkhani

Amanga womuganizira kuba chimanga

Bwalo la First Grade Magistrate ku Thyolo masiku apitawa lidagamula bambo Mphatso Mateyu, omwe amachokera m’mudzi mwa Changata, m’dera la T/A Changata m’bomalo, kuti akakhale ku ndende kwa zaka zitatu atamupeza wolakwa pa mlandu wakuba thumba la chimanga lolemera makilogalamu 50.

Bwalolo lidamva mlanduwo kudzera kwa woimira boma pa milandu, a Jailosi Phiri, amene adatsindika kuti bambo Mateyu adapalamula mlanduwo pa 25 April 2025, pamene iwo adabera bambo Ajison Nyozani, thumba lawo la chimanga cholemera makilogalamu 50 komanso kuwavulaza.

Iwo adapitiriza kufotokozera khotilo kuti a Nyozani adazindikira tsinzinantoleyo ngakhale panthawiyo adathawa, motero adapita kukamang’ala ku polisi ya Thyolo, zomwenso zidathandiza kuti bamboyo akwizingidwe unyolo msanga.

Ndipo woganiziridwayo atakaonekera ku bwalolo, a Mateyu adaukana mlanduwo ponena kutisadabe chimangacho ndiwo ngakhale kuvulaza mwini wakeyo. Izi zidachititsa kuti woimira boma pa milandu abweretse mboni zinayi.

Motero, umboni wochokera kwa mbonizo udakwanitsa kumupeza wolakwa bamboyo.

Podandaula, bambo Mateyu adapempha khotilo kuti liwamvere chisoni akamapereka chilango popeza iwo adachita za upanduzo chifukwa cha njala.

Koma woimira boma pa milandu adapempha bwalolo kuti lipereke chilango chokhwima chifukwa mchitidwe wakubawo ukuchulukirachulukirabe.

“Uku kudali ngati kupha popeza chaka chino kuli njala yadzaoneni choncho kuba sikungakhale njira yothetsera mavuto,” adatero iwo.

Popereka chigamulo, woweruza mlanduwo, a Kondwani Chinangwa, adagwirizana nawo a Phiri potsindika kuti mchitidwewo ukhoza kubweretsa chiwopsezo ndi mantha kwa anthu okhala m’bomalo.

Choncho, a Chinangwa adalamula bambo Mateyu kuti akakhale kundende kwa zaka zitatu, kutinso likhale phunziro kwa ena omwe ali ndi maganizo awupanduwo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button