Nkhani

Adagona ndi mwana, kapena ayi?

Zodulitsa mutu wa zizwa. Pomwe bwalo la milandu la majisitileti ku Mchinji lidagamula kuti a Ernest Chimpeni a zaka 37 akakhale ku ndende zaka 6 powaganizira kuti adagona ndi mwana, mkulu woimira boma pa milandu a Fostino Maele akamang’ala ku bwalo lalikulu la High Court ku Lilongwe kuti liunikirenso chigamulocho.

Izi zikudza kaamba koti ngakhale a Chimpeni adatsimikiza kuti adafuna kukwatira mtsikanayo chifukwa chitupa chake cha unzika chidasonyeza kuti ali ndi zaka 19, bwalolo lidawatumiza ku ndende chonsecho iwowo samadziwa kuti msungwanayo adanama zaka wandale wina atamuuza kuti akaname n’cholinga choti akavota pa Chisankho Chachikulu cha pa 16 September.

A Chimpeni, omwe adapereka K30 000 ndi nkhuku kwa makolo a mtsikanayo, adabweza magiya atapeza kuti adali kale ndi mimba.

Mneneri wapolisi ya Mchinji a Limbani Mpinganjira ati apolisi akusakabe mkulu adapereka mimba winayo, komanso wandale amene adauza mwanayo kuti aname zaka.

Potsatira chigamulocho, a Maele ati bwalo lalikulu liunikirenso bwino nkhaniyo potsatira gawo 138 (1) la malamulo a dziko lino. Izi zadulitsa mutu wa zizwa ena, pomwe akuona ngati pali kukhulana pakati pa a Maele ndi apolisi oimira boma pa milandu omwe ali pansi pawo.

Koma mneneri wa mlangizi wamkulu wa boma pa za malamulo a Frank Namangale, ati mkulu woimira boma pa mlandu akhonza kukamang’ala kuti bwalo lalikulu liunikirenso chigamulocho.

“Ndi zotheka ndithu kuti mkulu woimira boma pa milandu kufunsa bwalo lalikulu kuti liunikirenso chigamulo cha majisitireti ngati malamulo sanatsatidwe, chilungamo sichinayende ngati madzi kapena chilango chinali choposa mlingo. Monga zidakhalira ku Mchinji, zikusonyeza kuti mkulu woimira boma pa milandu akuona kuti bwalo lalikulu likhoza kusanthula chigamulocho,” adatero a Namangale.

Popereka chigamulo chawo, woweruza milandu a Godfrey Nyirenda adati kugwiritsa ntchito chiphaso cha unzika sikudali kokwanira potsimikizira zaka za msungwanayu kotero bamboyu anayenera kukagwira ukaidi wa kalavulagaga.

Koma pambuyo pa kuperekedwa kwa chigamulochi, magulu osiyasiyana kuphatikizapo woimira anthu pa milandu adasonyeza kusakondwa kwawo ndi mmene nkhaniyi idathera potengera kuti malamulo a dziko la Malawi amazindikira chiphaso cha unzika ngati umboni woti munthu adakwanitsa zaka 18.

Woimira anthu pa milandu a Silvester James Ayuba adati iye ndi wodzipereka kulowererapo pa nkhaniyi mwa ulere mpaka chilungamo chenicheni chitaoneka.

James Ayuba adati ndi zovuta kuti bwalo la milandu likakhulupirire umboni wa makolo a mtsikanayo.

“Tikufuna kutsata mlanduwu limodzi ndi mkulu woimira mlanduwu kuti bwalo lalikulu lisanthule ngati wozengedwa mlandu adalakwa kugwiritsa chitupa cha nzika chokha pofuna kudziwa zaka za mtsikanayo. Mbali inayi, tikhozanso kuchita apilo mlanduwo,” adatero iwo.

Bwalo lidamva kuti a Chimpeni adagona ndi mwanayo kuchokera mwezi wa March mpaka November chaka chatha kwa Kamwendo m’bomalo. Mayi a mwanayo, m’bwalo la milandu adati mwana wawo adabadwa pa 5 October 2008 ndipo adali wodabwa kuona kuti mwana wawo adalembetsa pa sukulu ya pulaimale ya Kamwendo Model kuti adabadwa pa 5 October 2008.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button