Samalani, kunjaku kwabuka cholera
Boma lalandira matamando pa momwe layendetsera dziko m’masiku 100 oyambirira koma malesawa akumana n’chipsinjo cha matenda a cholera omwe abuka ndipo afinya kwambiri maboma atatu mwa maboma 6 momwe apezeka.
Pofika Lachitatu lapitali, anthu 26 adali atatsimikizika kuti adagwidwa ndi cholera kuyambira pa 11 December 2025, mmodzi adamwalira nayo koma akadaulo ati chiwerengerochi chisatipusitse poti cholera imafala ngati moto wolusa.

A George Jobe omwe ndi mkulu wa bungwe loona kuti Amalawi akulandira thandizo la za umoyo moyenera la Malawi Health Equity Network (Mhen) ati kupanda kusamala, cholera ikhoza kugwira anthu mazanamazana tsiku limodzi.
“Cholera si matenda oyang’anira ayi chifukwa imafala mosanyengerera ikapeza mpata. Munthu mmodzi kupezeka ndi cholera ku dera ndiye kuti deralo lagwidwa ndi cholera chifukwa wapezekayo adanka ku chipatala koma komwe wachokako wasiyako bwanji?” Adatero a Jobe.
Iwo ati kufala kwa cholera sikutengera kulumidwa ngati malungo chifukwa munthu atha kutenga cholera kudzera m’chakudya, madzi akumwa zomwe timachita tsiku ndi tsiku.
“Cholera imangofuna kuti papezeke njira yoti tizirombo tisamuke pomwe tiliri n’kukapezeka m’chakudya kapena madzi akumwa basi koma ikangolowa m’thupi la munthu, nkhani yake imakhala kayakaya chifukwa imamwa madzi m’thupi,” atero a Jobe.
Malingana ndi bungwe loona za umoyo pa dziko lapansi la World Health Organization (WHO), cholera imafala kaamba ka kusowa ukhondo ndipo ngati yabuka m’dera, kufala kwake kumakhala kophweka.
Kadaulo wa za umoyo wa m’madera a Maziko Matemba ati kuthana ndi cholera n’kosavuta ngati anthu akutsatira malangizo akapewedwe makamaka kutsatira ukhondo m’mudzi, pa khomo ndi pa thupi.
“Mankhwala aakulu n’kupewa chifukwa cholera imasiyana ndi matenda ena omwe ukadwala umatha kulandira thandizo kwa kanthawi mpaka kuchira koma cholera ikakugwira, ukapanga tsoka umapita m’maola ochepa,” atero a Matemba.
Iwo ati momwe matendawa abuka chonchi, si bwino kudekha ngati kudera kwanu siidapezeke chifukwa n’kutheka kuti iliko koma siidapezeke chabe ndipo ikhoza kupezeka molusa kwambiri kaamba kakuchedwa kupezekako.
“Ngamwayi maboma omwe yapezeka kale chifukwa akhala tcheru koma kwa omwe siidapezeke, si nthawi yodekha chifukwa ikhoza kukhalako koma siikudziwika chabe ndipo podzapezeka ikhoza kudzakhala itaononga,” atero a Matemba.
Malingana ndi unduna wa za umoyo, zizindikiro za cholera n’kusanza komanso kuchita chimbudzi chofanana ndi madzi a mpunga ndipo mankhwala aakulu n’kumwa za madzimadzi poyembekeza thandizo la chipatala.
“Timalimbikitsa kuti anthu akaona zizindikiro zimenezi, azimpatsa mumthuyo za madzimadzi uku akumutengera ku chipatala kuti akataimikize ngati ilidi cholera. Choonde anthu asazengereze akaona izi,” atero olankhulira unduna wa za umoyo a Adrian Chikumbe.
Iwo ati pakadalipano, undunawo ukugwira ntchito limodzi ndi makhonsolo kuonetsetsa kuti matendawo asafalikire kwambiri ndipo atinso komiti yoona za miliri yayamba kale kukumana kuti ione za cholera.
Komitiyo ndi yomwe idakhazikitsidwa nyengo ya mliri wa Covid-19 ndipo idapatsidwanso udindo wolimbana ndi matenda a cholera omwe adavuta m’chaka cha 2023 pomwe adabuka nyengo yomwe anthu samayembekezera.
Anthu oposa 1 700 adamwalira ndi cholera yomwe idakhudza dziko lonse la Malawi pakati pa miyezi ya March 2022 ndi May 2023 pomwe komiti yoona za miliri idalengeza kuti kolerayo yachoka pa mlingo wa mliri.
Ena mwa maboma omwe cholera yapezeka kale ndi Kasungu komwe adapezeka anthu asanu, Neno komwe kudapezeka anthu atatu, Lilongwe, Balaka ndi Chitipa komwe kudapezeka munthu mmodzi kulikonse.



