Chichewa

Adasiya ntchito, koma ulimi

Munthu akafika poderera ntchito ndi kusankha ulimi ndiye kuti akupezamo phindu la mnanu. Magdalene Juma Mambiya wapeza chonde mu ulimi wa ziweto. Iye akuweta nkhuku, zinziri, nkhunda, nkhanga, abakha komanso nkhukutembo. BOBBY KABANGO walowa m’khola momwe akucheza ndi mlimiyo. Adacheza motere:

Mambiya amagogomoletsa mazira a nkhuku, zinziri

Tidziwane…

Ndine Magdalene Juma Mambiya, mwini wake wa MALJ Investments, kampani yomwe ikupanga zaulimi wa ziweto.

Chiyambi cha ulimiwu ndi chotani?

Chiyambi changa ndidali paofesi, ndagwirapo m’boma kwa zaka 33 ndipo ofesi yanga yomaliza idali ku Malawi Revenue Authority (MRA). Nditachoka uko ndidafunitsitsa ndiyike chidwi changa pa ulimi. Poyamba ndimakayikira chifukwa maphunziro anga ndi a Supply Chain ndiye zaulimi ndidalibe nazo luso kwenikweni. Koma nditayamba ndidaona kuti zimatheka ndipo mu 2016 ndi chaka chomwe ndidakhazikika mu ulimiwu.

Mukuwetachiyani?

Ndili ndi zinziri zoposa 5 000. Apapa ndili ndi mitundu ingapo ya zinziri monga mukuona zinazi ndi zazikulu kwambiri. Ndili ndi nkhuku za mikolongwe zokwana 2 300. Nkhuku za ‘kroiler’ zilipo 2 700 komanso nkhuku zalokolo zilipo 453. Ndilinso ndi abakha, nkhanga, nkhunda komanso nkhukutembo zomwe ndikugulitsa.

Chomwe mukugulitsa n’chiyani pamenepa?

Zonsezi anthu akabwera azipeza, chilichonse chomwe ndatchula apache anthu akazifuna adzazipeza koma panopa zomwe zikuyenda malonda ndi nkhuku mitundu yonse itatu.

Mazira mukugulitsanso?

Izo ndiye musakambe, kuyambira mwezi wa December akubwerayu nkhuku za mikolongwe zidzayamba kundipatsa mazira 2 000 pa tsiku chifukwa ndasunga kwambiri misoti. Panopa makolo okha akundipatsa mazira 600 patsiku. Nkhuku za makroilers panopa zikundipatsa mazira 450 patsiku komanso nkhuku zachikudazi zikundipatsa mazira 70 patsiku. Zinziri zikundipatsa mazira 400 patsiku, ndiye onsewa anthu akugula ndithu.

Anapiye mukugulitsanso?

Anapiye a zinziri komanso mtundu uliwonse wa nkhuku tikupezeka nawo chifukwa tili ndi incubator ziwiri zomwe tikufungatirira mazira onse. Incubator imodzi ikunyamula mazira 5 000.

Anthu amene akufuna ziwetozi abwere, sadzabwerera kuti zatha?

Koditu zomwe tikupanga kunoko ngakhale makampani atafika adzagula ndipo adzazilephera chifukwa tikuswetsa anapiye tsiku lililonse. Lero lokha tikuchezamu mwandipeza ndikutulutsa anapiye a mikolongwe 500 komanso mazira ena tafungatiritsa kale. Ofuna kugula atipeze kwa Kameza mumzinda wa Blantyre komanso timatumiza kulikonse chifukwa tapanga zida zomwe timanyamulira nkhuku.

Ntchito yonseyi mukugwira nokha?

Ayi ndithu sindingakwanitse, ndalemba anthu 5 amene akulandira pakutha pa mwezi. Awiri mwa iwo ndioti adatenga mapepala awo kusukulu ya Luanar. Amene akuyang’anira onsewa ndi Angela Meke wochokera ku Luanar. Panopa ndidapanga ubale ndi boma pamene amanditumizira ophunzira (interns) kuti adzaphunzire ntchito.

Ulimiwu wakupindulirani bwanji?

Galimoto zitatu zili apazi ndagula kuchokera mu ulimi omwewu. Makola onse mukuwaona apawa ndalama zake zikuchokera mu ulimiwu. Ana onse aphunzira sukulu zapamwamba ndipo onse akugwira ntchito, ulimiwu ndi kuyendetsa ndi amuna anga.

Related Articles

Back to top button