Chichewa

Akadaulo ayamikira ntchito Yochotsa zinyalala m’malawi

Listen to this article

Pamene mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera Lachitatu adakhazikitsa ntchito yoti Amalawi azichotsa zinyalala m’madera awo, akadaulo a zachilengedwe ati izi zifalikire ponseponse m’dziko muno.

Chakwera adakhazikitsa ntchito yoti Amalawi Lachisanu lachiwiri la mwezi ulionse azisesa ndi kuchotsa zinyalala m’madera awo kuyambira 3 koloko mpaka 5 koloko kuti kuwala kwa Malawi kubwerere m’chimake. Mwambowo udali kwa Chinsapo ku Lilongwe ndipo kudafika wachiwiri kwa mtsogoleriyo Saulos Chilima, nduna za boma, aphungu, akazembe a maiko ena ndi Amalawi ena.

Mtsogoleri wa bungwe la Movement for Environmental Action (MFEA) Matthews Malata komanso mmodzi mwa akuluakulu a bungwe la Centre for Environmental Policy and Advocacy (Cepa) Gloria Kamoto ayamikira boma pokhazikitsa chilinganizochi ndipo adati Amalawi onse ayenera kutengapo gawo kuti ntchitoyi isafere m’mazira

Chakwera kukankha wilibala ya zinyalala kwa Chinsapo

Malata adati pakufunika kuti boma likhazikitse thumba la ndalama lomwe ligwire ntchito yoonetsetsa kuti ntchitoyi ikuyenda bwino.

“Pakufunika kuti pakhazikitsidwe malamulo omwe azigwiritsidwa ntchito ndi makhonsolo poonetsetsa kuti aliyense akutsata ndondomeko pofuna kusamala Madera athu,” adatero Malata.

Iye adatinso mpofunikanso makampani omwe si aboma nawo azitenga mbali posamalira chilingedwe.

Kumbali yake, Kamoto adati pakufunika kuti Amalawi asinthe kaganizidwe poonetsetsa kuti malo omwe akukhala ndi aukhondo komanso otetezedwa.

“Akuluakulu a zipani akuyenera kupitirira kutenga mbali poonetsetsa kuti Malawi akuoneka waukhondo,” adatero Kamoto.

Iye adapempha makhonsolo kuti azichita zithu poyera pakagwiritsidwe ntchito ka ndalama zomwe ziyikidwe ku makhonsolo zoti zigwiritsidwe ntchito yosamalira malo isaonongedwe.

Kadaulo pa zachilengedwe Robert Kawiya adati boma likuyeneranso kuonetsetsa kuti makampani ndi mafakitale amene amataya zonyansa zochokera m’mafakitale awo m’mitsinje ya dziko lino kuti azipanidwa monga mwa lamulo.

“Mposavuta kuti makampaniwo azipanidwa chifukwa makhonsolo a m’mizinda ali ndi ogwira ntchito amene ntchito yawo ndi imeneyi. Makhonsolo akhala akugona posakwaniritsa ntchitozi,” adatero Kawiya.

Ndipo wapampando wa komiti yoona zachilengedwe Werani Chilenga adapempha eni mahotelo ndi malo ena okopa alendo kuti aziyesetsa kutolera mabotolo a pulasitiki amene amapezeka pafupi ndi malo awo.

Mneneri wa unduna owona zamaboma aang’ono Anjoya Mwanza adati undunawu ugwira ntchito ndi maunduna ena poonetsetsa kuti ntchitoyi ikuyenda bwino.

“Tayika adindo omwe aziyang’anira momwe ntchitoyi iziyendera komanso kuti undunawu uonetsetsa kuti zipangizo zonse zigawidwe nthawi yabwino,” adatero Mwanza.

Polankhulapo, Chakwera adati iyi ndi nthawi yoti Amalawi atengepo gawo kuti dziko lino libwerere kukhala lokongola.

“Ndili wokondwa chifukwa pakadalipano akukonza mabuliketi kuchoka kuzinyalala. Boma langa lithandiza kwambiri ntchito imeneyi,” adatero iye.

Ndipo dzulo, Chilima amayembekezeka kutenga nawo gawo pantchitoyi ku Ndirande mumzinda wa Blantyre.

Related Articles

Back to top button