Chichewa

Akhazikitsa lamulo Logonjetsera covid

Listen to this article

Boma lakhazikitsa lamulo lothandiza kulimbana ndi mlili wa Covid-19 loti akadaulo azaumoyo akuti ndi chida champhamvu pa nkhondo yolimbana ndi matendawa.

Lamulolo lakhazikitsidwa nyengo yomwe chiwerengero cha anthu opezeka ndi Covid-19 m’dziko muno chikuthamangira 5 000 ndipo ndichimodzi mwa ziwerengero zomwe zikuthamanga mu Africa.

Chiwerengero cha anthu opezeka ndi Covid-19 m’dziko muno chasuntha mwachangu kuchoka pa 1 038 ndi omwalira 13 malingana ndi zomwe udatulutsa unduna wazaumoyo pa June 27 2020 kufika 4 714 ndi omwalira 152 pa August 11 2020.

Izi zikutanthauza kuti pa mwezi umodzi ndi theka, chiwerengero cha opezeka ndi Covid-19 chaonjezekera ndi anthu 3 676 komanso omwalira 139.

Chiponda: Tikufuna kugonjeza Covid-19

 Malingana ndi nduna ya zaumoyo Khumbize Kandodo Chiponda, boma lidaona kuti n’chanzeru kuti likhazikitse lamulo lomwe lithandize polimbana ndi kukwera kwa chiwerengero cha anthu opezeka ndi matendawa.

“Sikuti lamuloli langobwera ayi, zidatengera kugundana mitu pakati pa unduna ndi nthambi zosiyanasiyana ndipo titakhutira kuti lamuloli likugwirizana ndi zolinga za dziko lino poteteza anthu ake ndipo tidalikhazikitsa pa August 8 2020,” adatero Chiponda.

Woimira boma pa milandu Chikosa Silungwe adati momwe zililimu chilichonse chatheka ndipo lamuloli lidayamba kale kugwira ntchito.

“Chomwe ndingapemphe n’choti anthu akhale ndi luntha lotsatira lamuloli chifukwa muli zilango zomwe opanga zosemphana nalo azilandira,” adatero Silungwe.

Zina zomwe lamulolo likunena n’zoti munthu akapezeka pagulu osavala masiki, azilipira ndalama zosachepera K10 000 kapena kukagwira ndende ya miyezi itatu.

Gawo lina likuti anthu sakuloledwa kukhala m’magulu a anthu oposa 10 ndipo misonkhano yonse yaletsedwa kupatula misonkhano yokhudza za Covid-19 basi.

 Milandu ina monga ya eni galimoto zonyamula anthu omwe akweza munthu wopanda masiki, eni malo ololeza anthu kuchitirako m’sonkhano woletsedwa, eni malo omwera mowa, komanso ophikira zakudya osatsata malamulo azilipira ndalama zosaposa K100 000 kapena kugwira ndende ya miyezi itatu.

Eni malo omwera mowa akuloledwa kutsegula kuyambira 2 koloko masana mpaka 8 koloko madzulo ndipo onse ofuna mowa azingogula n’kukamwera kwawo pamene amene ali ndi malo odyerapo azionetsetsa kuti anthu akukhala motalikirana pakudya kapena azingogula n’kukadyera kwina.

Gawo lina la lamuloli likupereka mphamvu kwa nthambi ya zachitetezo malingana ndi khumbo la nduna kugwiritsa ntchito mphamvu zilizonse zofuna kuti anthu atsatire lamuloli.

Pazamaliro, lamulolo likulola anthu osaposa 50 okha omwenso azidziteteza moyenera popita kumaliroko, koma pa za nyumba zopemphereramo Silungwe adangoti anthu asamaposemo 10.

Mneneri wapolisi James Kadadzera adati apolisi amasowa lamulo lowamasula manja kuti azigwira ntchito yawo yoonetsetsa kuti anthu akutsatira ndondomeko zopewera Covid-19.

“Apapa zakhala bwino chifukwa tsopano tili ndi lamulo lomwe tizigwiritsa ntchito.

“Tionetsetsa kuti anthu akutsatira lamuloli. Popanda lamulo ntchito yathu imavuta kagwiridwe kake,” adatero Kadadzera.

M’mwezi wa April 2020, boma lakale lidayesa kukhazikitsa ndondomeko zopewera Covid-19 zomwe ina idali ya m’bindikiro (lockdown) koma chifukwa padalibe lamulo lililonse, mabungwe ndi anthu ena adakatenga ziletso ndipo ndondomekozo sizidagwire ntchito.

Kadaulo pa zaumoyo Maziko Matemba wayamikira lamulo latsopanoli ponena kuti lipatsa mphamvu apolisi ndi asirikali ankhondo kugwiritsa ntchito mphamvu zomwe amalephera kutulutsa pankhondo yolimbana ndi Covid-19.

“Iyiyi si nkhondo ya masewera ayi ndi nkhondo yaikulu. Mungokumbukira momwe zidayendera m’maiko ena, tsono pamafunika kachikwapu kuti anthu azindikile kukula kwa nkhondoyi,” adatero Matemba.

Naye George Jobe wa bungwe la Malawi Health Equity Network (Mhen) adati kupatula kuphunzitsa anthu za Covid-19, lamuloli ligwira ntchito yaikulu bola anthu alimvetsetse.

Mafumu monga Maseya ya ku Chikwawa, Mponela ya ku Dowa, komanso Chikulamayembe ya ku Rumphi adati lamulolo lafika kale m’midzi ndipo mafumu ali kalikiliki kufotokozera anthu awo.

Maseya adati poti n’kumayambiriro anthu akumvetsetsa pang’onopang’ono za lamuloli moti ena akulephera kumvetsetsa chosiyira kupita kutchalitchi pamene ena akadali kumwera mowa m’malo ogulitsira momwe mukukhala khamu la anthu.

“Ukayenda m’ziphikomu, kukuoneka kuti anthu sadafike povomereza zomwe lamulo likunena pa zakamwedwe, koma poti mwina lamulo silidakhazikitse tiona,” adatero Maseya.

Mponela adati nkhani yayikulu yomwe ikuvuta ndi yamaliro chifukwa anthu adakhazikitsa mwambo wamaliro ngati chikhalidwe ndipo amalingalira za ulemu omwe maliro amayenera kulandira.

Related Articles

Back to top button