Nkhani

Akufuna chakudya ku Nsanje

Listen to this article

Ngakhale maboma ambiri zikuoneka kuti apata chakudya m’nyengo ya ulimi yangothayi, anthu ena m’boma la Nsanje ati akufuna thandizo la chakudya lomwe mabungwe ndi boma amapereka lipitirire kwa miyezi ina itatu chifukwa sanakolole chimanga chokwanira ndipo ali pa njala.

Phungu wa dera la kummwera kwa bomali, Thomson Kamangira, adanena izi pamsonkhano wa chitukuko omwe nduna yofalitsa nkhani Nicholas Dausi idachititsa podziwitsa anthu pulojekiti ya boma yoonetsetsa kuti netiweki ya lamya ikupezeka m’maboma onse mosavuta yotchedwa Malawi National Fibre Backbone sabata yatha.

Dausi: Tiyesetsa anthu asafe

Kamangira adati ng’amba yomwe inagwa chimanga chitangomasula ngayaye inasokoneza mbewu m’bomalo.

“Tikusowa zambiri koma pakali pano vuto ndi la njala. Izi ndi kaamba ka ng’amba osati madzi osefukira. Mabungwe asiya kupereka chakudya, koma tikuwapempha kupitiririza kwa miyezi itatu kuti tipulumuke ku njala yomwe itisause posachedwapa,” adatero Kamangira.

 Pothirira ndemanga, khansala Robert Chabvi adati anthu m’deralo chaka chinonso zawavuta kumunda ndipo boma ndi mabungwe awapase zida zochitira ulimi wamthirira.

“Sikuti ndife opemphetsa koma chimanga chatilakanso chaka chino. Boma ndi mabungwe tipatseni zida za ulimi wamthirira zoyendera mphamvu ya dzuwa kuti tilimenso uku mukutipatsa thandizo la chakudya. Pokhala kumudzi, anthu alibe chuma chogulira chimanga kwa mavenda kapena ku Admarc,” adatero Chabvi.

Poyankhapo, Dausi adati anthu asadere nkhawa chifukwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika achita zotheka kuti aliyense asafe ndi njala.

Izi zikusemphana ndi lipoti la boma la mu February lomwe linati chimanga chikololedwa chochuluka matani 3.2 miliyoni kusiyana ndi chaka chatha 2.3 miliyoni.

Malinga ndi mkulu wa Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira Banda nzosadabwitsa kuti anthu ena ku Nsanje adandaule za njala.

“Zolosera pa zokolola sizimasonyeza momwe zinthu zilili,” adatero iye.

Related Articles

Back to top button