Akuti akukumana Ndi womwalira

Maloza! Mtembo wa mtsikana uli m’nyumba, manda atakumbidwa, anthu ena amakumana naye akungozungulirazungulira pamsika komanso m’munda mwa makolo ake.

Anthu a m’mudzi mwa Mponda m’dera la mfumu Mduwa ku Mchinji komwe kwachitika nkhaniyi akuganiza kuti mtsikanayo, Violet Lubani, wa zaka 19 adachita kuphedwa m’masenga.

Katundu wambiri wa banjalo waotchedwa

Violet amadandaula kuti diso likumupweteka ndipo adapita naye ku Kamuzu Central Hospital ku Lilongwe komwe adamuchita opareshoni, koma adamwalirira patangopita masiku ochepa.

Nyakwawa ndi mafumu adauzidwa komanso anthu adafika mwaunyinji wawo kudzakhudza malirowo.

Gulupu Mponda ikuti maloza adayamba kuoneka mtembo wa mtsikanayo utayamba kutuluka thovu m’kamwa, m’makutu ndi m’phuno.

“Nkhope ndi nkhungu lake zimasintha. Nkhope yake imaoneka ngati ya mzimayi wachikulire kwambiri, pakapita nthawi  imaoneka ngati ya mwamuna.

“Nkhungu lake limayera pambuyo pake kuda kwambiri,” idafotokoza motero gulupuyo.

Anthu akudabwa ndi malozazo amayi omwe adapita kukathyola ndiwo zamasamba m’munda mwa makolo amtsikanayo adatulukamo chothawa.

“Adatifotokozera kuti akumana ndi malemuyo m’mundamo. Anthu adathamangira ku mundako, koma sadakampezemo.

“Tonse tinadabwa, komanso kugwidwa mantha. Mwambo wa maliro udapitirira ngakhale anthu ambiri sadakondwe ndi zomwe zimachitikazo,” adatero Mponda.

Chipwirikiti chidayamba anthu ena atabweranso ndi uthenga woti akumana ndi mtsikanayo kumsika.

“Titaona kuti adzukulu ndi anthu ena okwiya ndipo akukambirana zochitira mtopola makolowo powaganizira kuti akukhudzidwa ndi imfa ya mtsikanayo, tidazembetsa anamalirawo kuopa kuti anthu awachita chipongwe.

“Mafumu adaitanitsa apolisi kaamba koti zinthu zidafika poyipa,” adatero Mponda.

Anthu okwiya adagwetsa nyumba ndi kuotcha katundu wa banjalo moti mmene apolisi amafika zinthu zambiri zidali zitaonongeka kale.

Mneneri wapolisi wa m’boma la Mchinji, Rubrino Kaitano, adati adapeza ziwawa zili mkati moti sakadachoka mpaka kuonerera kuika mtembo wa Violet m’manda.

Violet adamwalira pa April 12 ndipo adaikidwa pa April 13.

Padakali pano apolisi atsekera m’chitokosi anthu oposa 13 kaamba kogumula nyumba zitatu ndi kuotcha katundu wa banjalo.

Mponda adati chiikireni malirowo m’manda “anthu ambiri akukumanabe ndi mtsikanayo m’malo osiyanasiyana”.

Msangulutso suudathe kulankhula ndi banjalo kaamba koti lachoka m’mudzimo, komanso komwe lalowera sikukudziwika. n

Share This Post