‘Ndidamuona koyamba mu Shoprite’

Kwangotsala sabata ziwiri zokha kuti anthu adzathyole dansi paphwando la ukwati wa Evance Mwale ndi Tiwonge Nundwe pa 4 May.

Evance amagwira ntchito ku Sinodi ya CCAP ya Livingstonia pomwe bwenzi lakelo ndi muulutsi pa wailesi ya Voice of Livingstonia.

Awiriwa akhala pa ubwenzi kwa zaka zitatu.

Chikondi cha Evans ndi Tiwonge chidazama kuntchito

Malinga ndi Mwale, adamuona koyamba Nundwe mu Shoprite ku Mzuzu, ndipo adamusangalatsa.

“Tidakumana koyamba m’chaka cha 2015 mu Shoprite ndipo adandipatsa chidwi mpaka ndidayamba kumufufuza ndithu kuti ndimudziwe bwino lomwe monga kwawo komanso kudziwa zomwe amachita,” adalongosola Mwale.

Ndipo iye adati anthu akufuna kwabwino adamuuza zonse za namwaliyu.

Komatu Mwale adali ndi mwayi chifukwa m’chaka chomwecho adapeza danga lokagwira ntchito kuofesi ya Nundwe komwe sadachitenso za bo! bo!bo! koma kuyamba kucheza ndi mtsikanayo.

Ndipo pofika chaka cha 2016, ubwenzi wa ponda-apa-nane-ndipondepo udayambika pakati pa awiriwa.

“Ndidamufunsira ndine chifukwa adalibe nane chidwi olo pang’ono kuti n’kukhala nane paubwenzi wokathera m’banja. Zidanditengera miyezi isanu ndi umodzi kuti andipatse danga lokhala naye pa ubwenzi,” adalongosola Mwale.

Komatu monga zikhalira, ubwenzi uliwonse umakhala ndi zokhoma zake ndipo nawo awiriwa akumana nazo zokhoma zofuna kuwalekanitsa, koma Chauta waikapo dzanja kuti amange banja.

Pomwe Mwale adamutsira diso Nundwe koyamba mu Shoprite, namwaliyo adamuona koyamba Mwale pomwe adakayamba kuphunzira ntchito kusinodiyi.

“Kumayambiliro timacheza monga munthu ndi mnzake, koma sindidaganizeko zoti awirife n’kukhala paubwenzi, koma ndi nthawi, tidayamba kucheza kwambiri mpaka anthu kumaona ngati tili paubwenzi pa nthawiyo, pomwe sizidali chomwechi,” adalongosola Nundwe.

Iye adati chikondi cha awiriwa chidayambira pomwe ankapitira limodzi kokadya nkhomaliro m’malo odyera mumzinda wa Mzuzu.

Mwale amachokera mmudzi wa Nkhunga kwa T/A Kanyenda, m’boma la Nkhotakota pamene Chikondi amachokera ku Hewe, T/A Katumbi, m’boma la Rumphi. n

Share This Post

Powered by