Nkhani

Amalawi apindulanji?

Listen to this article

Sabata yatha mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda adakhala wapampando wa bungwe la mgwirizano wa maiko a kumwera kwa Africa la Sadc. Izi zidadzetsa chimwemwe, polingaliranso kuti Banda ndi mayi woyamba kukhala wapampando wa bungweli.

Koma izi zili choncho, chiyembekezo cha Amalawi n’chakuti, kukhala wapampando kusangokhala kwa pakamwa chabe. Ubwino wa mpandowu ukuyenera kufikira anthu osaukitsitsa.

Dziko la Malawi silili palokha, choncho likhoza kupindula kwambiri ngati litalimbikitsa ubale wake ndi maiko ena m’dera lino la Africa. Mwachitsanzo, pali ntchito za mtengatenga, za magetsi, mayendedwe ndi zina zotere zimene dziko lino lingagwire mogwirizana ndi maiko ena.

Monga akufotokozera ena, doko la Nsanje litamalizidwa ndi bungwe la SADC likhoza kupindulira Amalawi.

Komanso pali nkhani yopala moto wa magetsi kuchoka ku Mozambique. Zonsezi zikhoza kuthandiza chitukuko cha dziko lino.

Mmbuyomu atsogoleri ena akhala ali pampando wotsogolera mabungwe osiyanasiyana koma palibe zolozeka zimene zimachitika ali pamipandoyo. N’chifukwa chake chiyembekezo chathu n’chachikulu kuti pamene Banda ndi wapampando wa Sadc, Amalawi nawo aphulapo kanthu.

Kupanda apo, nyimbo ikuimbiodwayi ikhala yowawasa chabe.

Related Articles

Back to top button