Nkhani

Amayi omwe ali ndi kachilombo akufuna mudzi wawo

Listen to this article

Amayi omwe ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ka HIV kwa T/A Kalolo ku Lilongwe apempha boma kuti liwapatse mudzi wawo kuti azipindula nawo pa ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo ya sabuside.

Amayiwa ati mafumu a m’midzi yomwe akukhala amawasala m’njira zambiri kuphatikizapo pa kagawidwe ka makuponi ogulira zipangizozi zomwe zimapangitsa kuti mabanja awo azikhala ndi njala chaka ndi chaka.

Iwo adapereka pempholi pamsonkhano omwe bungwe lowona za maufulu a anthu la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) lidakonza kumudzi wa Kalolo ku Lilongweko kuti amaiwa akumane ndi akuluakulu osiyanasiyana kuti apereke madandaulo awo pazovuta zomwe amakumana nazo.

Mkulu wa gulu lina la amayi omwe ali ndi kachilombo la Kalolo Community Aids Coordinating Committee Tisauke Nazoni wati amaiwa amaphonya kamwedwe ka mankhwala obwezeretsa chitetezo m’thupi, ma ARV, chifukwa chosowa chakudya zomwe zimaika miyoyo yawo pachiopsezo.

“N’zokhumudwitsa kuona kuti makuponi akuperekedwa kwa anthu oti ali ndi mphamvu oti akhoza kudzipezera zipangizo mosavuta koma tikati tiyesere kudandaula amati tipalamula. Ma ARV amafunika chakudya chokwanira koma nthawi zina timalephera kumwa chifukwa palibe chakudya. Timatha kukhala ndi njala kuyambira m’mawa mpaka madzulo,” adatero Nazoni.

Koma woyendetsa ntchito zaulimi ku Chileka EPA komwe amaiwa amachokera Chrissie Chiusiwa wati pempho la amaiwo silingatheke chifukwa midzi yolandira zipangizozi imatengera malire a ma T/A omwe amapereka ndondomeko kuboma.

Iye adapempha amaiwo kuti akadandaule kuofesi yoyendetsa za ulimi kapena kuofesi ya bwanamkubwa wa Lilongwe kuti akawathandize.

Mfumu yaikulu Sakuzamutu idavomereza kuti mafumu ang’onoang’ono ena amachita za chinyengo, kupondereza anthu.

Iye adati aitanitsa mafumu onse kuti akhale nawo pansi ndi kukambirana nawo kuti mchitidwewu uthe.

“Ndizachisoni chifukwa anthu ngati amenewa ndiamene boma limaganizira m’mapologalamu ngati awa a sabuside tsono ngati mafumu akutenga zinthuzi ndikumagawira anthu amphamvu kale ndiye kuti tikuchitapo chiyani? Tikhala nawo pasi kuti tikonze zonse,” adatero Sakuzamutu.

Related Articles

Back to top button
Translate »