Chichewa

Anatchereza

Listen to this article

Ndipite kwa asing’anga?

Zikomo Anatchereza,

Palitu mkazi amene amandizunguza bongo. Mtima wanga nthawi zonse umakhala pa iye ndipo sindigona tulo chifukwa cha kukongola ngakhalenso khalidwe lake labwino.

Koma nthawi zonse ndikamufunsira amandikana. Ndipo safuna kumva za ine.

Pamene zafikapa, ndikulingalira zolowera kwa asing’anga. Ndilakwitsa?

MDP,

Chiradzulu.

Zikomo baba,

Zimatheka kuti munthu amene umamukonda, iye osakukonda n’komwe. Ndine mmodzi mwa amene sakhulupirira zopita kwa asing’anga. Izi zili choncho makamaka chifukwa choti zoyambira kwa asing’anga nthawi zambiri zimakathera komweko.

Ndamvapo za anthu ofuna kulemera atapita kwa asing’anga koma chifukwa cholephera kukwaniritsa zizimba n’kubwerera kwa sing’anga yomweyo chifukwa apenga misala.

Inde, ndamvapo za amayi ofuna kuti amuna awo akhuzumuke ndipo azikhala pakhomo, koma mpaka kuyambanso kuwakola zedi, kukana kupita kuntchito ati chifukwa zakufuna kutalikana ndi akazi awo!

Nthawi zina abambo amafunsira munthu woti sangayanjane naye. Mupeze mwamuna kulimbikira kufunsira mkazi wamaphunziro a pamwamba zedi, kapena wa chuma kwambiri chonsecho iwo ndi a kapunthabuye. Mundimvetsetse, chikondi sichiona chuma kapena maphunziro komatu kumadziwa kuti mkazi uyu tikulingana.

Kodi mungapite pamsika kufuna ng’ombe muli ndi ndalama zokwanira nkhuku yokha?

Zonse zili apo, muyeneranso kudziwa kuti mwina akazi ena amalola munthu amene akuoneka kuti sakungofuna kuwayesa chabe. Muyenera kudzisanthula chifukwa n’kutheka kuti muli ndi kachibwana kenakake kamene kangachititse kuti mkazi akusaseni.

MDP,

Chiradzulu

Ndikusowa wosankha

Agogo,

Ndili ndi zibwenzi zitatu ndipo ndimafuna kudzakwatirapo mmodzi. Vuto limene lilipo ndi loti onsewo akuoneka kuti amandikonda ndipo ndikusowa wosankha. Inenso ndimawakonda onsewo. Ndichite chiyani?

AJ,

Lilongwe.

Zikomo AJ,

Zikuonekeratu kuti inuyo simunakonzeke kumanga banja ndi munthu. Sizingatheke munthu mmodzi kukonda akazi atatu osiyana molingana.

Zikuoneka kuti mukadali m’chipululu ndipo ndi pempho langa kuti bakhalni momwemo.

Koma chomwe ndingakulangizeni n’choti kunjaku kudaopsa ndipo masewera ochita paulimbo otere nthawi yake idatha kalekale.

Mudalakwa kuchita zibwenzi ndi akazi onsewo, mumafuna kupeza chiyani? Muthetsa bwanji zibwenzi zinazo n’kutsala ndi mmodzi?

Komanso mwangoonetseratu kuti ndinu wosakhulupirika chifukwa mudafunsira akazi ena chonsecho mudali ndi ena pambali. Zonse zili apo, mwakhala nthawi yonseyi mukupusitsa akazi onsewo choncho n’zosamveka kuti lero mukusowa wosankha. Mtima wanu ndi wa chimasomaso.

Ofuna mabanja

Ndili ndi zaka 33 ndipo ndikufuna mkazi, akhale wa pantchito, woyera m’maonekedwe komanso wa zaka za pakati pa 25 ndi 30. 0886142309

Ndikufuna shuga mami, ochokera ku Lilongwe. 0990058710 /0884873246

Related Articles

Back to top button