Chichewa

Njiru yafika pena

Listen to this article

Bambo wina wa zaka 30, ali m’chitokosi cha apolisi pomuganizira kuti adapha mwana wake wa zaka 7, ku Chileka mumzinda wa Blantyre.

Dziwani Banda akumuganizira kupha mwana wake Christopher Banda, Lamulungu pa 15 August.

Izi zachitika apolisi ku Machinjiri mumzinda wa Blantyre omwewo atatsekeranso mayi wina pamodzi ndi sing’anga powaganizira kuti adapha mwana wa mayiyo wa zaka 11 ndi kumukwilira ku mpanda wa nyumba yawo.

Ndipo sabata yatha yomwewo, apolisi ku Zomba adamanga mayi wina pamodzinso ndi mwamuna wake powaganizira kuti adapha mwana wawo wa zaka ziwiri pomukankha kuchoka pakhonde ndipo adamukwirira usiku m’munda wina ku Zomba komweko.

Izi zachitikanso patangodutsa sabata zochepa, apolisi m’boma la Dedza atatsekera bambo wina pomuganizira kuti adapha mwana womupeza wa zaka zitatu pomwe mkazi wake adali ku bizinesi.

Ana ngati awa ali ndi ufulu wokhala ndi moyo

Kafukufuku yemwe Msangulutso wapanga pa nkhani zokhudza kupha anaku ukuonetsa kuti ambiri mwa anawa, akuphedwa ndi makolo owapeza.

Mwachitsanzo, mwa ana asanu omwe aphedwa, atatu akuganiziridwa kuti adaphedwa ndi bambo owapeza.

Mneneri wa polisi ku Chileka, Peter Mchiza, watsimikiza za nkhaniyi ndipo adati Banda yemwe amakhala m’mudzi mwa Jamali, Mfumu Chigalu, m’boma la Blantyre adampeza mwana wakeyo yemwe adali ndi zaka 4 akusewera pamjingo, m’mudzi mwa M’bwana.

Iye adati apa Banda adamtengera mwanayo kumalo komwe mpaka lero sadauze anthu ndipo sadabwelere naye.

“Pomwe anthu adamufunsa komwe adasiya mwanayo, Banda adakanika kuyankha zomveka bwino,” adalongosola Mchiza.

Koma Mchiza adati apa abale ake ena adakatula nkhaniyi kupolisi ya Lirangwe ndipo thupi la Christopher lidapezeka litakwiriridwa m’chitsime china m’mudzi mwa Jamali Lolemba pa August 16.

Iye adati achipatala adapeza kuti mwanayo adafa pomupotokola khosi.

“Tidamutsekera Banda ndikumutsekulira mlandu wakupha munthu,” adalongosola Mchiza.

Khalidweli silidasiye malo chifukwa nako ku Chitipa, bambo wina ali m’manja mwa apolisi pomuganizira kuti adapha mwana womupeza wa zaka ziwiri.

Izi zidachitika m’mudzi mwa Njebete, Mfumu Mwenemisuku m’bomalo.

Polankhulapo, mneneri wa polisi m’bomalo Gladwell Simwaka adati Wayuyo Pwele wa zaka 18, akuganiziridwa kuti adapha mwanayo Lusekelo Banda, pomupotokola pakhosi.

“Pwele wakhala pa banja ndi mayi wa mwanayo dzina lake Mirriam Mushiko kwa miyezi 7, ndipo mtsikanayu ali ndi pathupi pa miyezi isanu,” adatero Simwaka.

Iye adati koma Pwele samamufuna mwanayo pakhomopo ndipo adamuuza mkazi wakeyo kuti amutumize kwa agogo ake, zomwe zidabweretsa mapokoso pa awiriwo.

Malinga ndi Simwaka, Pwele akumuganizira kuti adapha mwanayo pomwe amachokera kumowa.

“Mkazi wake adayesera kulowererapo, koma Pwele adamutibula, ndi kumuthamangitsa pakhomopo. Anthu a chifundo adayesa kumutengera mwanayu kuchipatala cha Misuku, komwe adakafika naye atafa kale,” Simwaka adatero.

Pakadalipano, Pwele akuyankha mlandu wopha munthu.

Related Articles

Back to top button
Translate »